Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Estere 5:3 - Buku Lopatulika

3 Ninena naye mfumu, Mufunanji, Estere mkazi wamkulu? Pempho lanu nchiyani? Lidzaperekedwa kwa inu, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumuwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ninena naye mfumu, Mufunanji, Estere mkazi wamkulu? Pempho lanu nchiyani? Lidzaperekedwa kwa inu, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumuwo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Kenaka mfumu inati kwa iye, “Kodi mukufuna chiyani, inu mfumukazi Estere? Nanga pempho lanu ndi chiyani? Ngakhale mutapempha theka la ufumu, ndidzakupatsani.”

Onani mutuwo Koperani




Estere 5:3
11 Mawu Ofanana  

Pamenepo mkaziyo anati, Ndikupemphani kapempho kamodzi, musandikaniza. Ndipo mfumu inati kwa iye, Tapemphani amai wanga, popeza sindikukanizani.


Ku Gibiyoni Yehova anaonekera Solomoni m'kulota usiku, nati Mulungu, Tapempha chimene ndikupatse.


Ndipo mfumu inati kwa ine, Ufunanji iwe? Pamenepo ndinapemphera Mulungu wa Kumwamba.


Ndipo Estere anati, Chikakomera mfumu, adze mfumu ndi Hamani lero ku madyerero ndinawakonzera.


Ndipo mfumu inati kwa Estere pa madyerero a vinyo, Pempho lanu nchiyani? Lidzaperekedwa kwa inu; mufunanji? Chidzachitika, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumuwo.


Nitinso mfumu kwa Estere tsiku lachiwirili pa madyerero a vinyo, Pempho lanu nchiyani, mkazi wamkulu Estere? Lidzapatsidwa kwa inu; mufunanji? Chidzachitika, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumu wanga.


Ndipo mfumu inati kwa mkazi wamkulu Estere, Ayuda adapha, naononga amuna mazana asanu m'chinyumba cha ku Susa, ndi ana aamuna khumi a Hamani; nanga m'maiko ena a mfumu munachitikanji? Pempho lanu ndi chiyani tsono? Lidzachitikira inu; kapena mufunanjinso? Kudzachitika.


Ndipo anamlumbirira iye, kuti, Chilichonse ukandipempha ndidzakupatsa, kungakhale kukugawira ufumu wanga.


Ufuna ndikuchitire chiyani? Ndipo anati, Ambuye, kuti ndipenyenso.


Ndipo kapitao wamkulu anamgwira dzanja, napita naye padera, namfunsa m'tseri, Chiyani ichi uli nacho kundifotokozera?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa