Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Estere 4:6 - Buku Lopatulika

6 Natuluka Hataki kunka kwa Mordekai kukhwalala la mzinda linali popenyana ndi chipata cha mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Natuluka Hataki kunka kwa Mordekai kukhwalala la mudzi linali popenyana ndi chipata cha mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Choncho Hataki anapita kwa Mordekai ku bwalo la mzinda patsogolo pa chipata cha mfumu.

Onani mutuwo Koperani




Estere 4:6
5 Mawu Ofanana  

Ndi m'maiko monse, paliponse anafikapo mau a mfumu ndi lamulo lake, panali maliro aakulu mwa Ayuda, ndi kusala, ndi kulira misozi, ndi kubuma; nagona m'chiguduli ndi mapulusa ambiri.


Pamenepo Estere anaitana Hataki mdindo wina wa mfumu, amene idamuika amtumikire, namuuza amuke kwa Mordekai, kuti adziwe ichi nchiyani ndi chifukwa chake ninji.


Ndipo Mordekai anamfotokozera zonse zidamgwera, ndi mtengo wake wa ndalama adati Hamani adzapereka m'nyumba ya chuma cha mfumu pa Ayuda, kuwaononga.


Nitinso mfumu kwa Estere tsiku lachiwirili pa madyerero a vinyo, Pempho lanu nchiyani, mkazi wamkulu Estere? Lidzapatsidwa kwa inu; mufunanji? Chidzachitika, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumu wanga.


Ndipo mfumu inati kwa mkazi wamkulu Estere, Ayuda adapha, naononga amuna mazana asanu m'chinyumba cha ku Susa, ndi ana aamuna khumi a Hamani; nanga m'maiko ena a mfumu munachitikanji? Pempho lanu ndi chiyani tsono? Lidzachitikira inu; kapena mufunanjinso? Kudzachitika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa