Estere 4:3 - Buku Lopatulika3 Ndi m'maiko monse, paliponse anafikapo mau a mfumu ndi lamulo lake, panali maliro aakulu mwa Ayuda, ndi kusala, ndi kulira misozi, ndi kubuma; nagona m'chiguduli ndi mapulusa ambiri. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Ndi m'maiko monse, paliponse anafikapo mau a mfumu ndi lamulo lake, panali maliro akulu mwa Ayuda, ndi kusala, ndi kulira misozi, ndi kubuma; nagona m'chiguduli ndi mapulusa ambiri. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Chigawo chilichonse kumene mawu a mfumu ndi lamulo lake zinafika, kunali maliro akulu pakati pa Ayuda. Iwo ankasala zakudya, kulira mofuwula ndi kumadandaula. Ambiri anavala ziguduli ndi kudzola phulusa. Onani mutuwo |
Pamenepo anaitana alembi a mfumu mwezi woyamba, tsiku lake lakhumi ndi chitatu, nalembera monga mwa zonse Hamani analamulira akazembe ndi ziwanga zoyang'anira maiko ali onse, ndi akalonga a mitundu iliyonse ya anthu, maiko ali onse monga mwa chilembedwe chao, ndi mitundu iliyonse ya anthu monga mwa chinenedwe chao; anazilemba m'dzina la mfumu Ahasuwero, nazisindikiza ndi mphete ya mfumu.