Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Estere 2:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo iye adalera Hadasa, ndiye Estere, mwana wamkazi wa atate wake wamng'ono; popeza iye analibe atate kapena amai; ndi namwaliyo anali wa maonekedwe okoma, ndi wokongola; ndipo atamwalira atate wake ndi mai wake, Mordekai anamtenga akhale mwana wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo iye adalera Hadasa, ndiye Estere, mwana wamkazi wa atate wake wamng'ono; popeza iye analibe atate kapena amai; ndi namwaliyo anali wa maonekedwe okoma, ndi wokongola; ndipo atamwalira atate wake ndi mai wake, Mordekai anamtenga akhale mwana wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Mordekai nʼkuti atalera Hadasa, amene ankatchedwanso Estere, mwana wamkazi wa amalume ake chifukwa analibe abambo kapena amayi. Mtsikanayu anali wokongola ndi wooneka bwino ndipo Mordekai ankamutenga ngati mwana wake weniweni pamene abambo ndi amayi ake anamwalira.

Onani mutuwo Koperani




Estere 2:7
12 Mawu Ofanana  

Tsopano ana ako aamuna awiri, amene anakubadwira iwe m'dziko la Ejipito, ndisanadze kwa iwe ku Ejipito, ndiwo anga; Efuremu ndi Manase, monga Rubeni ndi Simeoni, ndiwo anga.


abwere naye Vasiti mkazi wamkulu pamaso pa mfumu ndi korona wachifumu, kuonetsa anthu ndi akulu kukoma kwake; popeza anali wokongola maonekedwe ake.


Pofika tsono kulowa kwake kwa Estere mwana wa Abihaili, atate wamng'ono wa Mordekai, amene adadzitengera akhale mwana wake, kuti alowe kwa mfumu, sanafune kanthu koma zonena Hegai mdindo wa mfumu wosunga akazi ndizo. Ndipo Estere anayamikizidwa pamaso pa onse ompenya.


Estere sadawulule chibale chake kapena mtundu wake, monga Mordekai adamuuza; popeza Estere anachita mau a Mordekai monga m'mene analeredwa naye.


Tsiku lomwelo mfumu Ahasuwero anampatsa mkazi wamkulu Estere nyumba ya Hamani mdani wa Ayuda. Nafika Mordekai pamaso pa mfumu; pakuti Estere adamuuza za chibale chake.


kapena kudya nthongo yanga ndekha, osadyako mwana wamasiye;


(pakuti kuyambira ubwana wanga analeredwa ndi ine monga ndi atate; ndipo ndinakhala nkhoswe ya wamasiye chibadwire ine.)


ndipo ndidzakhala kwa inu Atate, ndi inu mudzakhala kwa Ine ana aamuna ndi aakazi, anena Ambuye Wamphamvuyonse.


Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m'maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.


Taonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tili ife otere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa