Estere 2:16 - Buku Lopatulika16 Momwemo anatengedwa Estere kunka kwa mfumu Ahasuwero, kunyumba yake yachifumu, mwezi wakhumi, ndiwo mwezi wa Tebeti, chaka chachisanu ndi chiwiri cha ufumu wake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Momwemo anatengedwa Estere kunka kwa mfumu Ahasuwero, kunyumba yake yachifumu, mwezi wakhumi, ndiwo mwezi wa Tebeti, chaka chachisanu ndi chiwiri cha ufumu wake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Anapita naye kwa mfumu Ahasiwero ku nyumba ya ufumu pa mwezi wa khumi, mwezi wa Tebete, chaka cha chisanu ndi chiwiri cha ufumu wake. Onani mutuwo |
Pamenepo anaitana alembi a mfumu nthawi yomweyo, mwezi wachitatu, ndiwo mwezi wa Sivani, tsiku lake la makumi awiri ndi chitatu, monga mwa zonse Mordekai analamulira; nalembera kwa Ayuda, ndi kwa akazembe, ndi ziwanga, ndi akalonga a kumaiko, oyambira ku Indiya, ofikira ku Kusi, maiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri, ku dziko lililonse monga mwa chilembedwe chao, ndi mtundu uliwonse monga mwa chinenedwe chao, ndi kwa Ayuda monga mwa chinenedwe chao.