Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Estere 2:12 - Buku Lopatulika

12 Kunafika tsono kulowa kwake kwa namwali aliyense, kuti alowe kwa mfumu Ahasuwero, atamchitira monga mwa lamulo la akazi, miyezi khumi ndi iwiri; pakuti ankakwaniritsa masiku a mayeretsedwe ao motero, miyezi isanu ndi umodzi ndi mafuta a mure, ndi miyezi isanu ndi umodzi ndi zonunkhira bwino, ndi zoyeretsa akazi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Kunafika tsono kulowa kwake kwa namwali aliyense, kuti alowe kwa mfumu Ahasuwero, atamchitira monga mwa lamulo la akazi, miyezi khumi ndi iwiri; pakuti ankakwaniritsa masiku a mayeretsedwe ao motero, miyezi isanu ndi umodzi ndi mafuta a mure, ndi miyezi isanu ndi umodzi ndi zonunkhira bwino, ndi zoyeretsa akazi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Tsono nthawi inkafika kuti namwali aliyense akaonekere kwa mfumu Ahasiwero, pakutha pa miyezi khumi ndi iwiri yomwe inakhazikitsidwa kuti amayi azidzikongoletsa. Pa miyezi isanu ndi umodzi ankadzola mafuta a mure ndipo pa miyezi isanu ndi umodzi inayo ankadzola zonunkhira ndi zokongoletsa.

Onani mutuwo Koperani




Estere 2:12
10 Mawu Ofanana  

Ndi Mordekai akayendayenda tsiku ndi tsiku kubwalo la nyumba ya akazi, kuti adziwe umo akhalira Estere, ndi chimene chidzamchitikira.


Ndipo namwali aliyense analowa kwa mfumu motero, zilizonse anafuna anampatsa zochokera m'nyumba ya akazi, alowe nazo kunyumba ya mfumu.


ndi mfumu aike oyang'anira m'maiko onse a ufumu wake, kuti asonkhanitse anamwali onse okongola m'chinyumba cha ku Susa, m'nyumba ya akazi; awasunge Hegai mdindo wa mfumu wosungira akazi, nawapatse zowayeretsa;


Ndipo namwaliyo anamkomera, namchitira chifundo; ndipo anafulumira kumpatsa zake zomyeretsa, ndi magawo ake, ndi anamwali asanu ndi awiri oyenera kumpatsa ochokera m'nyumba ya mfumu; ndipo anamsuntha iye ndi anamwali ake akhale m'malo okometsetsa m'nyumba ya akazi.


ndakapiza pamphasa panga mankhwala onunkhira a mure ndi chisiyo ndi sinamoni.


Ndaniyu akwera kutuluka m'chipululu ngati utsi wa tolo, wonunkhira ndi mure ndi lubani, ndi zonunkhiritsa zonse za wogulitsa?


Ndipo padzakhala m'malo mwa zonunkhiritsa mudzakhala zovunda; ndi m'malo mwa lamba chingwe; ndipo m'malo mwa tsitsi labwino dazi; m'malo mwa chovala chapachifuwa mpango wachiguduli; zipsera m'malo mwa ukoma.


Ndipo unanka kwa mfumu, utadzola mafuta ndi kuchulukitsa zonunkhira zako; ndipo unatumiza atumwi ako kutali; ndipo wadzichepetsa wekha kufikira kunsi kumanda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa