Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Estere 10:2 - Buku Lopatulika

2 Ndi zochita zonse za mphamvu yake, ndi nyonga zake, ndi mafotokozedwe a ukulu wa Mordekai, umene mfumu inamkulitsa nao, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Mediya ndi Persiya?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndi zochita zonse za mphamvu yake, ndi nyonga zake, ndi mafotokozedwe a ukulu wa Mordekai, umene mfumu inamkulitsa nao, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Mediya ndi Persiya?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ndipo ntchito zonse zochitika ndi mphamvu zake komanso ndi zonse zofotokoza za ukulu wa Mordekai, kukwezedwa kwake ndi mfumu, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Mediya ndi Peresiya?

Onani mutuwo Koperani




Estere 10:2
10 Mawu Ofanana  

Ndipo machitidwe otsiriza a Solomoni, ndi ntchito zake zonse anazichita, ndi nzeru zake, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a Solomoni?


Ndipo machitidwe ena a Yerobowamu m'mene umo anachitira ufumu, taona, analembedwa m'buku la machitidwe a mafumu a Israele.


Tsono machitidwe ena a Ahabu, ndi zonse adazichita, ndi nyumba ya minyanga adaimanga, ndi mizinda yonse adaimanga, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele?


Ndipo atafunsira mlanduwo, anaupeza momwemo, napachikidwa onse awiri pamtengo; ndipo anachilemba m'buku la mbiri pamaso pa mfumu.


Usiku uja tulo tidamwazikira mfumu, niti abwere nalo buku la mbiri, naliwerenga pamaso pa mfumu.


Ndipo Mordekai anatuluka pamaso pa mfumu wovala chovala chachifumu chamadzi ndi choyera, ndi korona wamkulu wagolide, ndi malaya abafuta ndi ofiirira; ndi mzinda wa Susa unafuula ndi kukondwera.


Ndipo mfumu inavula mphete yake adailanda kwa Hamani, naipereka kwa Mordekai. Ndi Estere anaika Mordekai akhale woyang'anira nyumba ya Hamani.


Pakuti Mordekai anali wamkulu m'nyumba ya mfumu, ndi mbiri yake idabuka m'maiko onse; pakuti munthuyu Mordekai anakulakulabe.


Ndipo mwandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu; ndipo dzanja lamanja lanu landigwiriziza, ndipo chifatso chanu chandikuza ine.


Pamenepo mfumu inasandutsa Daniele wamkulu, nimpatsa mphatso zazikulu zambiri, namlamuliritsa dera lonse la ku Babiloni; nakhala iye kazembe wamkulu wa anzeru onse a ku Babiloni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa