Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Estere 1:16 - Buku Lopatulika

16 Ndi Memukana anati, pamaso pa mfumu ndi akalonga, Vasiti mkazi wamkulu sanalakwire mfumu yekha, komanso akalonga onse, ndi mitundu yonse ya anthu okhala m'maiko onse a mfumu Ahasuwero.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndi Memukana anati, pamaso pa mfumu ndi akalonga, Vasiti mkazi wamkulu sanalakwire mfumu yekha, komanso akalonga onse, ndi mitundu yonse ya anthu okhala m'maiko onse a mfumu Ahasuwero.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Ndipo Memukani anayankha pa maso pa mfumu ndi olemekezeka anzake kuti, “Mfumukazi Vasiti sanalakwire mfumu yokha, koma walakwiranso olemekezeka onse ndi anthu onse okhala mʼzigawo zonse za mfumu Ahasiwero.

Onani mutuwo Koperani




Estere 1:16
6 Mawu Ofanana  

Ndipo pokhala mfumu Ahasuwero, poyambira ufumu wake, analembera chowaneneza okhala mu Yuda ndi mu Yerusalemu.


Anati, Tidzachitanji naye mkazi wamkulu Vasiti monga mwa malamulo, popeza sanachite chomuuza mfumu Ahasuwero mwa adindo?


Pakuti machitidwe awa a mkazi wamkuluyo adzabuka kufikira akazi onse, kupeputsa amuna ao pamaso pao; anthu akati, Mfumu Ahasuwero anati abwere naye Vasiti mkazi wamkulu pamaso pake, koma sanadze iye.


Koma pamene Paulo anati atsegule pakamwa pake, Galio anati kwa Ayuda, Ukadakhala mlandu wa chosalungama, kapena dumbo loipa, Ayuda inu, mwenzi nditakumverani inu;


Koma Paulo anati, Ndilikuimirira pa mpando wachiweruziro wa Kaisara, pompano ndiyenera kuweruzidwa ine; Ayuda sindinawachitire kanthu koipa, monga mudziwanso nokha bwino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa