Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 35:26 - Buku Lopatulika

26 Ndi akazi onse ofulumidwa mtima ndi luso anapota ubweyawo wa mbuzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Ndi akazi onse ofulumidwa mtima ndi luso anapota ubweyawo wa mbuzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Akazi onse alusowo adaombanso nsalu za ubweya wambuzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Ndipo amayi onse amene anali ndi mtima wofuna ndipo anali ndi luso analuka ubweya wa mbuzi.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 35:26
8 Mawu Ofanana  

Nagamula nyumba za anyamata adama okhala kunyumba ya Yehova, kumene akazi anaomba nsalu zolenjeka za chifanizocho.


Ndipo anadza, aliyense wofulumidwa mtima, ndi yense mzimu wake wamfunitsa, nabwera nacho chopereka cha Yehova, cha ku ntchito ya chihema chokomanako, ndi ku utumiki wake wonse, ndi ku zovala zopatulika.


Ndi akazi onse a mtima waluso anapota ndi manja ao, nabwera nalo thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.


Ndi akulu anabwera nayo miyala yasohamu, ndi miyala yoti aiike kuefodi, ndi kuchapachifuwa;


Amuna ndi akazi onse a ana a Israele amene mitima yao inawafunitsa eni kubwera nazo za ku ntchito yonse imene Yehova analamula ipangike ndi dzanja la Mose, anabwera nacho chopereka chaufulu, kuchipereka kwa Yehova.


Ndipo Mose adaitana Bezalele ndi Oholiyabu, ndi anthu onse aluso, amene Yehova adaika luso m'mtima mwao, onse ofulumidwa mtima ayandikize kuntchito kuichita.


Ndipo onse a mtima waluso mwa iwo akuchita ntchitoyi anapanga chihema ndi nsalu zophimba khumi; anaziomba ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi akerubi, ntchito ya mmisiri.


Agwira njinga ya thonje ndi dzanja lake, nafumbata mtengo wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa