Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 35:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo anadza, aliyense wofulumidwa mtima, ndi yense mzimu wake wamfunitsa, nabwera nacho chopereka cha Yehova, cha ku ntchito ya chihema chokomanako, ndi ku utumiki wake wonse, ndi ku zovala zopatulika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo anadza, aliyense wofulumidwa mtima, ndi yense mzimu wake wamfunitsa, nabwera nacho chopereka cha Yehova, cha ku ntchito ya chihema chokomanako, ndi ku utumiki wake wonse, ndi ku zovala zopatulika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Ndipo munthu aliyense, monga momwe mtima wake unkafunira, adabwera kwa Chauta ndi zopereka zopangira chihema chamsonkhano cha Chauta. Adabwera nazo zonse zogwiritsira ntchito potumikira, ndi zonse zopangira zovala zopatulika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 ndipo aliyense amene anakhudzidwa mu mtima mwake nafuna kupereka, anabwera kudzapereka chopereka kwa Yehova cha ntchito yokonza tenti ya msonkhano, cha ntchito zonse za mʼtentimo ndi cha zovala zopatulika.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 35:21
28 Mawu Ofanana  

Pakuti inu, Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, munawulula kwa mnyamata wanu kuti, Ndidzakumangira iwe nyumba; chifukwa chake mnyamata wanu analimbika mtima kupemphera pemphero ili kwa Inu.


Ndipo mfumu Davide anaima chilili, nati, Mundimvere ine, abale anga ndi anthu anga, ine kumtima kwanga ndinafuna kulimangira likasa la chipangano la Yehova, ndi popondapo mapazi a Mulungu wathu nyumba yopumulira, ndipo ndidakonzeratu za nyumbayi.


Ndipo iwe Solomoni mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna Iye udzampeza, koma ukamsiya Iye adzakusiya kosatha.


Koma ndine yani, ndi anthu anga ndiwo ayani, kuti tidzakhoza kupereka mwaufulu motere? Popeza zonsezi zifuma kwanu; takupatsani zofuma ku dzanja lanu.


Ndiponso popeza ndikondwera nayo nyumba ya Mulungu wanga, chuma changachanga cha golide ndi siliva ndili nacho ndichipereka kunyumba ya Mulungu wanga, moonjezera ndi zonse ndazikonzeratu nyumba yopatulikayo;


Ndipo amene anali nayo miyala ya mtengo wake anaipereka ku chuma cha nyumba ya Yehova, mwa dzanja la Yehiyele Mgeresoni.


Ndipo anthu anakondwera popeza anapereka mwaufulu; pakuti ndi mtima wangwiro anapereka mwaufulu kwa Yehova; mfumu Davide yemwe anakondwera ndi chimwemwe chachikulu.


Ndipo akulu ena a nyumba za makolo, pofika kunyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu, anapereka chaufulu kwa nyumba ya Mulungu chakuiimika pakuzika pake.


Wodala Yehova Mulungu wa makolo athu, amene anaika chinthu chotere mu mtima wa mfumu, kukometsera nyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu,


Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu: M'moyera mokometsetsa, mobadwira matanda kucha, muli nao mame a ubwana wanu.


Lankhula ndi ana a Israele, kuti anditengere chopereka; ulandire chopereka changa kwa munthu aliyense mtima wake umfunitsa mwini.


Ndipo khamu lonse la ana a Israele linachoka pamaso pa Mose.


Ndipo anadza amuna ndi akazi, onse akufuna mtima eni ake, nabwera nazo mphete za mphuno, mphete za m'makutu, ndi mphete zosindikizira, ndi zigwinjiri, zonsezi zokometsera za golide; inde yense wakupereka kwa Yehova chopereka chagolide.


Ndi akazi onse ofulumidwa mtima ndi luso anapota ubweyawo wa mbuzi.


Amuna ndi akazi onse a ana a Israele amene mitima yao inawafunitsa eni kubwera nazo za ku ntchito yonse imene Yehova analamula ipangike ndi dzanja la Mose, anabwera nacho chopereka chaufulu, kuchipereka kwa Yehova.


Mumtengere Yehova chopereka cha mwa zanu; aliyense wa mtima womfunitsa mwini abwere nacho, ndicho chopereka cha Yehova; golide, ndi siliva, ndi mkuwa;


Ndipo Mose adaitana Bezalele ndi Oholiyabu, ndi anthu onse aluso, amene Yehova adaika luso m'mtima mwao, onse ofulumidwa mtima ayandikize kuntchito kuichita.


Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.


Ndipo mkulu wao adzakhala mwa iwo, ndi wolamulira wao adzatuluka pakati pao; ndipo ndidzamyandikitsa iye, ndipo adzayandikira kwa Ine, pakuti iye wolimba mtima kuyandikira kwa Ine ndani? Ati Yehova.


Akubadwa inu a njoka, mungathe bwanji kulankhula zabwino, inu akukhala oipa? Pakuti m'kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima.


Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa.


Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.


Galamuka, Debora, galamuka, galamuka, galamuka, unene nyimbo; uka, Baraki, manga nsinga ndende zako, mwana wa Abinowamu, iwe.


Imvani mafumu inu; tcherani makutu, akalonga inu; ndidzamuimbira ine Yehova, inetu; ndidzamuimbira nyimbo, Yehova, Mulungu wa Israele.


Mtima wanga uvomerezana nao olamulira a mu Israele, amene anadzipereka mwaufulu mwa anthu. Lemekezani Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa