Eksodo 25:33 - Buku Lopatulika33 Ku mphanda ina kukhale zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi duwa; ndi ku mphanda inzake zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi duwa; zitere mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m'choikaponyalicho. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201433 Ku mphanda ina kukhale zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa; ndi ku mphanda inzake zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa; zitere mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m'choikapo nyalicho. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa33 Mphanda yoyamba ikhale ndi zikho zitatu zopangidwa ngati maluŵa amtowo, nkhunje ndi duŵa. Ku mphanda ina kukhalenso zikho zitatu zonga maluŵa amtowo, nkhunje ndi duŵa. Zikhale momwemo mphanda zonse zisanu ndi imodzi zotuluka m'choikaponyalecho. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero33 Zikho zitatu zokhala ngati za maluwa amtowo, mphukira ndi duwa zikhale pa mphanda yoyamba. Pa mphanda yachiwiri pakhalenso zikho zitatu zokhala ngati za maluwa amtowo, mphukira ndi duwa. Ndipo mphanda zonse zisanu ndi imodzi zikhale chimodzimodzi ndipo zituluke mʼchoyikapo nyalecho. Onani mutuwo |