Chivumbulutso 9:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo mngelo wachisanu anaomba lipenga, ndipo ndinaona nyenyezi yochokera kumwamba idagwa padziko; ndipo anampatsa iye chifunguliro cha chiphompho chakuya. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo mngelo wachisanu anaomba lipenga, ndipo ndinaona nyenyezi yochokera kumwamba idagwa padziko; ndipo anampatsa iye chifunguliro cha chiphompho chakuya. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Pamenepo mngelo wachisanu adaliza lipenga lake. Atatero ndidaona nyenyezi itagwa pansi kuchokera ku thambo. Idapatsidwa kiyi ya dzenje lopita ku Chiphompho chakuya. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Mngelo wachisanu anayimba lipenga lake, ndipo ndinaona nyenyezi ikugwa pa dziko lapansi kuchokera ku thambo. Nyenyeziyo inapatsidwa kiyi ya ku chidzenje chakuya. Onani mutuwo |
Chilombo chimene unachiona chinaliko, koma kulibe; ndipo chidzatuluka m'chiphompho chakuya, ndi kunka kuchitayiko. Ndipo adzazizwa iwo akukhala padziko amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo chiyambire makhazikidwe a dziko lapansi, pakuona chilombo, kuti chinaliko, ndipo kulibe, ndipo chidzakhalako.