Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 8:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachisanu ndi chiwiri, munali chete mu Mwamba monga mwa nthawi ya ora latheka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachisanu ndi chiwiri, munali chete m'Mwamba monga mwa nthawi ya ora latheka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pomaliza Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachisanu ndi chiŵiri. Pamenepo onse Kumwamba adangoti chete pa hafu la ora.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Atatsekula chomatira chachisanu ndi chiwiri, kumwamba kunakhala chete mphindi makumi atatu.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 8:1
14 Mawu Ofanana  

Unaima chilili, koma sindinathe kuzindikira maonekedwe ake; panali mzukwa pamaso panga; kunali chete, ndipo ndidamva mau akuti,


Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye; usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m'njira yake, chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu.


Moyo wanga ukhalira chete Mulungu yekha; chipulumutso changa chifuma kwa Iye.


Koma Yehova ali mu Kachisi wake wopatulika; dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake.


Khalani chete, anthu onse, pamaso pa Yehova; pakuti wagalamuka mokhalira mwake mopatulika.


Ndipo iwo anamuka, nasunga manda, nasindikizapo chizindikiro pamwalapo, iwo pamodzi ndi alondawo.


Ndipo ndinaona m'dzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wachifumu buku lolembedwa m'kati ndi kunja kwake, losindikizika ndi zizindikiro zisanu ndi ziwiri.


Ndipo aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,


Ndipo ndinaona pamene Mwanawankhosa anamasula chimodzi cha zizindikiro zisanu ndi ziwiri, ndipo ndinamva chimodzi mwa zamoyo zinai, chikunena, ngati mau a bingu, Idza.


Ndipo ndinaona pamene anamasula chizindikiro chachisanu ndi chimodzi, ndipo panali chivomezi chachikulu; ndi dzuwa lidada bii longa chiguduli cha ubweya ndi mwezi wonse unakhala ngati mwazi;


Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachiwiri, ndinamva chamoyo chachiwiri chikunena, Idza.


Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachitatu, ndinamva chamoyo chachitatu chikunena, Idza. Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wakuda; ndipo iye womkwera anali nao muyeso m'dzanja lake.


Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachinai, ndinamva mau a chamoyo chachinai chikunena, Idza.


Ndipo pamene adamasula chizindikiro chachisanu, ndinaona pansi pa guwa la nsembe mizimu ya iwo adaphedwa chifukwa cha mau a Mulungu, ndi chifukwa cha umboni umene anali nao:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa