Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Chivumbulutso 7:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo ndinamva chiwerengo cha iwo osindikizidwa chizindikiro, zikwi makumi khumi ndi makumi anai mphambu anai, osindikizidwa chizindikiro mwa mafuko onse a ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo ndinamva chiwerengo cha iwo osindikizidwa chizindikiro, zikwi makumi khumi ndi makumi anai mphambu anai, osindikizidwa chizindikiro mwa mafuko onse a ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Tsono ndidamva chiŵerengero cha olembedwa chizindikiro aja. Chidakwanira zikwi 144, ndipo olembedwa chizindikirowo anali a m'fuko lililonse la Aisraele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Choncho ndinamva chiwerengero cha amene ankayenera kulembedwa chizindikiro aja. Analipo okwanira 144,000 kuchokera ku mafuko onse a Israeli.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 7:4
17 Mawu Ofanana  

Ndipo anamtulutsa iye kunja, nati, Tayang'anatu kumwamba, uwerenge nyenyezi, ngati ukhoza kuziwerenga zimenezo: ndipo anati kwa iye, Zoterezo zidzakhala mbeu zako.


Ndi miyalayi ikhale monga mwa maina a ana a Israele, khumi ndi awiri, monga maina ao; monga malochedwe a chosindikizira, yonse ikhale monga maina ao, kwa mafuko khumi ndi awiri.


Atero Ambuye Yehova, Malire amene mugawe nao dziko likhale cholowa chao monga mwa mafuko khumi ndi awiri a Israele ndi awa: Yosefe akhale nao magawo awiri.


Iwo ogwira ntchito m'mzinda mwa mafuko onse a Israele alimeko.


ndi zipata za mzinda zidzakhala monga mwa maina a mafuko a Israele; zipata zitatu kumpoto: chipata chimodzi cha Rubeni, chipata chimodzi cha Yuda, chipata chimodzi cha Levi;


Katundu wa mau a Yehova padziko la Hadaraki, ndipo Damasiko adzakhala popumula pake; pakuti Yehova apenyerera anthu monga apenyerera mafuko onse a Israele;


Ndipo Yesu anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti inu amene munanditsata Ine, m'kubadwanso, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iwiri, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israele.


Ndipo kapoloyo anati, Ambuye, chimene munachilamulira chachitika, ndipo malo atsalapo.


ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu ndi kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israele.


kufikira komweko mafuko athu khumi ndi awiri, potumikira Mulungu kosapumula usiku ndi usana, ayembekeza kufikirako. Chifukwa cha chiyembekezo ichi, Mfumu, andinenera Ayuda.


Ndipo Yesaya afuula za Israele, kuti, Ungakhale unyinji wa ana a Israele ukhala monga mchenga wa kunyanja, chotsalira ndicho chidzapulumuka.


Yakobo, kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, kwa mafuko khumi ndi awiri a m'chibalaliko: ndikupatsani moni.


Ndipo ndinapenya, taonani, Mwanawankhosayo alikuimirira paphiri la Ziyoni, ndipo pamodzi ndi Iye zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, akukhala nalo dzina lake ndi dzina la Atate wake lolembedwa pamphumi pao.


ndipo aimba ngati nyimbo yatsopano kumpando wachifumu, ndi pamaso pa zamoyo zinai, ndi akulu; ndipo palibe munthu anakhoza kuphunzira nyimboyi, koma zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, ogulidwa kuchokera kudziko.


Mwa fuko la Yuda anasindikizidwa chizindikiro zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Rubeni zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Gadi zikwi khumi ndi ziwiri.


Ndipo chiwerengero cha nkhondo za apakavalo ndicho zikwi makumi awiri zochulukitsa zikwi khumi; ndinamva chiwerengero chao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa