Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 7:1 - Buku Lopatulika

1 Zitatha izi ndinaona angelo anai alinkuimirira pangodya zinai za dziko, akugwira mphepo zinai za dziko, kuti ingaombe mphepo padziko, kapena panyanja, kapena pa mtengo uliwonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Zitatha izi ndinaona angelo anai alinkuimirira pangodya zinai za dziko, akugwira mphepo zinai za dziko, kuti ingaombe mphepo padziko, kapena panyanja, kapena pa mtengo uliwonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pambuyo pake ndidaona angelo anai ataimirira pa mbali zinai za dziko lapansi. Anali atagwira mphepo zinai za dziko lapansi kuti ndi imodzi yomwe isaombe pa dziko, kapena pa nyanja, kapena pa mtengo uliwonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Zitatha izi ndinaona angelo anayi atayima pa mbali zinayi za dziko lapansi, atagwira mphepo zinayi za dziko lapansi kuletsa kuti mphepo iliyonse isawombe pa dziko kapena pa nyanja kapena pa mtengo uliwonse.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 7:1
23 Mawu Ofanana  

Ndipo Iye adzaimika mbendera ya amitundu, ndipo adzasonkhanitsa oingitsidwa a Israele, namema obalalika a Yuda, kuchokera kumadera anai a dziko lapansi.


Ine Yehova ndiusunga uwo; ndidzauthirira madzi nthawi zonse; ndidzausunga usiku ndi usana, kuti angauipse.


Munalimbana naye pang'ono, pamene munamchotsa; wamchotsa iye kuomba kwake kolimba tsiku la mphepo yamlumbanyanja.


Pa Elamu ndidzatengera mphepo zinai kumbali zinai za mlengalenga, ndidzamwaza iwo kumphepo zonsezo; ndipo sikudzakhala mtundu kumene opirikitsidwa a Elamu sadzafikako.


Ndipo anati kwa ine, Nenera kwa mpweya, nenera, wobadwa ndi munthu iwe, nuti kwa mpweya, Atero Ambuye Yehova, Idza, mpweya iwe, kuchokera kumphepo zinai, nuuzire ophedwa awa, kuti akhale ndi moyo.


Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, atero Ambuye Yehova kwa dziko la Israele, Kwatha; kwafika kutha kwake pangodya zinai za dziko.


Ndipo pakuuka iye ufumu wake udzathyoledwa, nudzagawikira kumphepo zinai za mlengalenga; koma sadzaulandira a mbumba yake akudza m'mbuyo, kapena monga mwa ulamuliro wake anachita ufumu nao; pakuti ufumu wake udzazulidwa, ukhale wa ena, si wa aja ai.


Daniele ananena, nati, Ndinaona m'masomphenya anga usiku, taonani, mphepo zinai za mumlengalenga zinabuka pa nyanja yaikulu.


Ndipo tondeyo anadzikulitsa kwakukulu, koma atakhala wamphamvu, nyanga yake yaikulu inathyoka; ndi m'malo mwake munaphuka nyanga zinai zooneka bwino, zoloza kumphepo zinai za mlengalenga.


Koma Yehova anautsa chimphepo chachikulu panyanja, ndipo panali namondwe wamkulu panyanja, ndi chombo chikadasweka.


Ndipo ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anatuluka magaleta anai pakati pa mapiri awiri; ndi mapiriwo ndiwo mapiri amkuwa.


Ndi mthenga anayankha, nati kwa ine, Izi ndi mphepo zinai zakumwamba zakutuluka kumene zimaimirira pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi.


Ndipo Iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwakukulu kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kumphepo zinai, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ake ena.


Ndipo pamenepo adzatuma angelo, nadzasonkhanitsa osankhidwa ake ochokera kumphepo zinai, kuyambira ku malekezero ake a dziko lapansi, ndi kufikira ku malekezero a thambo.


nadzatuluka kudzasokeretsa amitundu ali mungodya zinai za dziko, Gogi, ndi Magogi, kudzawasonkhanitsa achite nkhondo: chiwerengero chao cha iwo amene chikhala ngati mchenga wa kunyanja.


Ndipo ndinamva ngati mau pakati pa zamoyo zinai, nanena, Muyeso wa tirigu wogula rupiya, ndi miyeso itatu ya barele yogula rupiya; ndi mafuta ndi vinyo usaziipse.


nanena, Musaipse dziko, kapena nyanja, kapena mitengo, kufikira tidasindikiza chizindikiro akapolo a Mulungu wathu, pamphumi pao.


Ndipo woyamba anaomba lipenga, ndipo panakhala matalala ndi moto, zosakaniza ndi mwazi, ndipo anazitaya padziko lapansi; ndipo limodzi la magawo atatu a dziko lidapserera, ndipo limodzi la magawo atatu a mitengo lidapserera, ndipo msipu wonse udapserera.


nanena kwa mngelo wachisanu ndi chimodzi wakukhala ndi lipenga, Masula angelo anai omangidwa pamtsinje waukulu Yufurate.


Ndipo ananena kwa ilo kuti lisaipse udzu wa padziko, kapena chabiriwiri chilichonse, kapena mtengo uliwonse, koma anthu amene alibe chizindikiro cha Mulungu pamphumi pao ndiwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa