Chivumbulutso 6:9 - Buku Lopatulika9 Ndipo pamene adamasula chizindikiro chachisanu, ndinaona pansi pa guwa la nsembe mizimu ya iwo adaphedwa chifukwa cha mau a Mulungu, ndi chifukwa cha umboni umene anali nao: Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Ndipo pamene adamasula chizindikiro chachisanu, ndinaona pansi pa guwa la nsembe mizimu ya iwo adaphedwa chifukwa cha mau a Mulungu, ndi chifukwa cha umboni umene anali nao: Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Zitatha izi, Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachisanu. Ndipo ndidaona kunsi kwa guwa lansembe mizimu ya anthu amene adaphedwa chifukwa cha kulalika mau a Mulungu, ndiponso chifukwa chochitira mauwo umboni wamphamvu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachisanu, ndinaona kunsi kwa guwa lansembe kunali mizimu ya anthu amene anaphedwa chifukwa cha Mawu a Mulungu ndi chifukwa chochitira umboni. Onani mutuwo |
Ndipo ndinaona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambire chilombo, kapena fano lake, nisanalandire lembalo pamphumi ndi padzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Khristu zaka chikwi.