Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Chivumbulutso 5:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo ndinaona mngelo wamphamvu wakulalikira ndi mau aakulu, Ayenera ndani kutsegula buku, ndi kumasula zizindikiro zake?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo ndinaona mngelo wamphamvu wakulalikira ndi mau akulu, Ayenera ndani kutsegula buku, ndi kumasula zizindikiro zake?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Kenaka ndidaona mngelo wamphamvu akufunsa mokweza mau kuti, “Ndani ali woyenera kufutukula bukuli ndi kumatula zimatiro zake?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ndipo ndinaona mngelo wamphamvu akulengeza ndi mawu okweza kuti, “Ndani ali woyenera kumatula zomatira ndi kufutukula bukuli?”

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 5:2
8 Mawu Ofanana  

Mamba ake olimba ndiwo kudzitama kwake; amangika pamodzi ngati okomeredwatu.


Lemekezani Yehova, inu angelo ake; a mphamvu zolimba, akuchita mau ake, akumvera liu la mau ake.


Ndipo ndinaona mngelo wina wolimba alikutsika Kumwamba, wovala mtambo; ndi utawaleza pamutu pake, ndi nkhope yake ngati dzuwa, ndi mapazi ake ngati mizati yamoto;


Ndipo mngelo wolimba ananyamula mwala ngati mphero yaikulu, naiponya m'nyanja, nanena, Chotero Babiloni, mzinda waukulu, udzapasulidwa kolimba, ndipo sudzapezedwanso konse.


Ndipo ndinaona m'dzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wachifumu buku lolembedwa m'kati ndi kunja kwake, losindikizika ndi zizindikiro zisanu ndi ziwiri.


ndipo mmodzi wa akulu ananena ndi ine, Usalire: taona, Mkango wochokera m'fuko la Yuda, Muzu wa Davide, wapambana kuti akhoza kutsegula buku ndi zizindikiro zake zisanu ndi ziwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa