Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 5:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo ndinaona m'dzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wachifumu buku lolembedwa m'kati ndi kunja kwake, losindikizika ndi zizindikiro zisanu ndi ziwiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo ndinaona m'dzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wachifumu buku lolembedwa m'kati ndi kunja kwake, losindikizika ndi zizindikiro zisanu ndi ziwiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pambuyo pake ndidaona buku m'dzanja lamanja la wokhala pa mpando wachifumu uja. Bukulo linali lolembedwa m'kati ndi kumbuyo komwe, ndipo linali lomatidwa ndi zimatiro zisanu ndi ziŵiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Kenaka ndinaona buku mʼdzanja la wokhala pa mpando waufumu uja. Bukulo linali lolembedwa mbali zonse ndipo linali lomatidwa ndi zomatira zisanu ndi ziwiri.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 5:1
16 Mawu Ofanana  

Ndipo masomphenya onse akusandukirani mau a m'buku limatidwa ndi phula, limene anthu amapereka kwa wina wodziwa kuwerenga, nati, Werengani umu; koma ati, Sindingathe, chifukwa lamatidwa ndi phula;


Funani inu m'buku la Yehova, nimuwerenge; palibe umodzi wa iye udzasowa, palibe umodzi udzasowa unzake; pakuti pakamwa pa Yehova panena, ndipo mzimu wake wasonkhanitsa iwo.


Manga umboni, mata chizindikiro pachilamulo mwa ophunzira anga.


Ndipo masomphenya a madzulo ndi mamawa adanenawo ndi oona; koma iwe ubise masomphenyawo, popeza adzachitika atapita masiku ambiri.


Pamenepo ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, taonani, mpukutu wouluka.


ndipo anali nako m'dzanja lake kabuku kofunyulula: ndipo anaponda nalo phazi lake lamanja panyanja, ndi lamanzerelo pamtunda,


ndipo maonekedwe a Iye wokhalapo anafanana ndi mwala wa jaspi, ndi sardiyo; ndipo panali utawaleza wozinga mpando wachifumu, maonekedwe ake ngati smaragido.


Ndipo pamene zamoyozo zipereka ulemerero ndi ulemu ndi uyamiko kwa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, kwa Iye wakukhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi,


Ndipo cholengedwa chilichonse chili m'mwamba, ndi padziko, ndi pansi padziko, ndi m'nyanja, ndi zonse zili momwemo, ndinazimva zilikunena, Kwa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa zikhale chiyamiko, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi mphamvu, kufikira nthawi za nthawi.


Ndipo anadza, nalitenga kudzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wachifumu.


Ndipo ndinaona pamene Mwanawankhosa anamasula chimodzi cha zizindikiro zisanu ndi ziwiri, ndipo ndinamva chimodzi mwa zamoyo zinai, chikunena, ngati mau a bingu, Idza.


nanena kwa mapiri ndi matanthwe, Igwani pa ife, ndipo tibiseni ife kunkhope ya Iye amene akhala pa mpando wachifumu, ndi kumkwiyo wa Mwanawankhosa;


Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachisanu ndi chiwiri, munali chete mu Mwamba monga mwa nthawi ya ora latheka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa