Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 3:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Filadelfiya lemba: Izi anena Iye amene ali Woyera, Iye amene ali Woona, Iye wakukhala nacho chifungulo cha Davide, Iye wotsegula, ndipo palibe wina atseka; Iye wotseka, ndipo palibe wina atsegula:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Filadelfiya lemba: Izi anena Iye amene ali Woyera, Iye amene ali Woona, Iye wakukhala nacho chifungulo cha Davide, Iye wotsegula, ndipo palibe wina atseka; Iye wotseka, ndipo palibe wina atsegula:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 “Mtsogoleri wa mpingo wa ku Filadelfiya umlembere kuti, Naŵa mau ochokera kwa Iye amene ali woyera ndi woona, amene ali ndi kiyi yaulamuliro ya Mfumu Davide. Uja amene amati akatsekula, palibe wotinso nkutseka, ndipo akatseka, palibe wotinso nkutsekula.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 “Lembera mngelo wampingo wa ku Filadefiya kuti: Awa ndi mawu ochokera kwa amene ndi woyera ndi woonadi, amene ali ndi kiyi ya Davide. Iye akatsekula palibe amene angatseke; ndipo akatseka palibe amene angatsekule.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 3:7
38 Mawu Ofanana  

Akapita, nakatsekera, nakatulutsa bwalo la mlandu, adzamletsa ndani?


Taona, agamula, ndipo palibe kumanganso; amtsekera munthu, ndipo palibe kumtsegulira.


Yehova ali wolungama m'njira zake zonse, ndi wachifundo m'ntchito zake zonse.


Pakuti simudzasiya moyo wanga kumanda; simudzalola wokondedwa wanu avunde.


Pakuti chikopa chathu chifuma kwa Yehova; ndi mfumu yathu kwa Woyera wa Israele.


Ndipo ndidzaika mfungulo wa nyumba ya Davide paphewa pake, ndipo iye adzatsegula, ndipo palibe wina adzatseka, iye adzatseka ndipo palibe wina adzatsegula.


chokani inu munjira, patukani m'bande, tiletsereni Woyera wa Israele pamaso pathu.


Usaope, Yakobo, nyongolotsi iwe, ndi anthu inu a Israele; ndidzakuthangata iwe, ati Yehova, ndiye Mombolo wako, Woyera wa Israele.


Iwe udzawapeta, ndi mphepo idzawauluza; ndipo kamvulumvulu adzawamwaza; ndipo iwe udzasangalala mwa Yehova, udzadzikuza mwa Woyera wa Israele.


kuti iwo aone ndi kudziwa, ndi kulingalira, ndi kumvetsa pamodzi, kuti dzanja la Yehova lachita ichi, ndipo Woyera wa Israele wachilenga ichi.


Mombolo wathu, Yehova wa makamu ndi dzina lake, Woyera wa Israele.


Atero Yehova, Mombolo wako, Woyera wa Israele, Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m'njira yoyenera iwe kupitamo.


Atero Yehova, Mombolo wa Israele, ndi Woyera wake, kwa Iye amene anthu amnyoza, kwa Iye amene mtundu wathu unyasidwa naye, kwa mtumiki wa olamulira: Mafumu adzaona, nadzauka; akalonga nadzalambira chifukwa cha Yehova, amene ali wokhulupirika, ngakhale Woyera wa Israele, amene anakusankha Iwe.


Pakuti Mlengi wako ndiye mwamuna wako; Yehova wa makamu ndiye dzina lake; ndi Woyera wa Israele ndiye Mombolo wako; Iye adzatchedwa Mulungu wa dziko lonse lapansi.


Taona, iwe udzaitana mtundu umene sunaudziwe, ndi mtundu umene sunakudziwe udzakuthamangira, chifukwa cha Yehova Mulungu wako, ndi chifukwa cha Woyera wa Israele; pakuti Iye wakukometsa.


Ndipo wina anafuula kwa mnzake, nati, Woyera, Woyera, Woyera, Yehova wa makamu; dziko lonse lapansi ladzala ulemerero wake.


Ndidzakupatsa mafungulo a Ufumu wa Kumwamba; ndipo chimene ukamanga padziko lapansi chidzakhala chomangidwa Kumwamba: ndipo chimene ukachimasula padziko lapansi, chidzakhala chomasulidwa Kumwamba.


Thambo ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mau anga sadzachoka ai.


Kuti, Tili ndi chiyani ife ndi Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadza kudzationonga ife: Ndikudziwani, ndinu Woyerayo wa Mulungu.


Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulukulu: ndipo Ambuye Mulungu adzampatsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake:


Ha! Tili ndi chiyani ndi Inu, Yesu wa ku Nazarete? Kodi munadza kutiononga ife? Ndikudziwani Inu muli yani, ndinu Woyera wake wa Mulungu.


Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.


Koma inu munakaniza Woyera ndi Wolungamayo, ndipo munapempha kuti munthu wambanda apatsidwe kwa inu,


Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.


ndi kuti, Chimene upenya, lemba m'buku, nulitumize kwa Mipingo isanu ndi iwiri, ku Efeso, ndi ku Smirina, ndi ku Pergamo, ndi ku Tiatira, ndi ku Sardi, ndi ku Filadelfiya, ndi ku Laodikea.


ndi Wamoyoyo; ndipo ndinali wakufa, ndipo taona, ndili wamoyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo ndili nazo zofungulira za imfa ndi dziko la akufa.


ndi kwa Yesu Khristu, mboni yokhulupirikayo, wobadwa woyamba wa akufa, ndi mkulu wa mafumu a dziko lapansi. Kwa Iye amene atikonda ife, natimasula kumachimo athu ndi mwazi wake;


Ndipo aimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha.


Ndipo ndinamva wa paguwa la nsembe, alinkunena, Inde, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, maweruziro anu ali oona ndi olungama.


Ndipo ndinaona mutatseguka mu Mwamba; ndipo taonani, kavalo woyera, ndi Iye wakumkwera wotchedwa Wokhulupirika ndi Woona; ndipo aweruza, nachita nkhondo molungama.


pakuti maweruzo ake ali oona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene anaipsa dziko ndi chigololo chake, ndipo anabwezera chilango mwazi wa akapolo ake padzanja lake la mkaziyo.


Kwa mngelo wa Mpingo wa ku Efeso lemba: Izi azinena Iye amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziwiri m'dzanja lake lamanja, Iye amene ayenda pakati pa zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide:


Ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu anati, Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano. Ndipo ananena, Talemba; pakuti mau awa ali okhulupirika ndi oona.


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Laodikea lemba: Izi anena Ameni'yo, mboni yokhulupirika ndi yoona, woyamba wa chilengo cha Mulungu:


Ndipo zamoyozo zinai, chonse pa chokha chinali nao mapiko asanu ndi limodzi; ndipo zinadzala ndi maso pozinga ponse ndi m'katimo; ndipo sizipumula usana ndi usiku, ndi kunena, Woyera, woyera, woyera, Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, amene anali, amene ali, ndi amene alinkudza.


Ndipo aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,


ndipo anafuula ndi mau aakulu, ndi kunena, Kufikira liti, Mfumu yoyera ndi yoona, muleka kuweruza ndi kubwezera chilango chifukwa cha mwazi wathu, pa iwo akukhala padziko?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa