Chivumbulutso 3:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Sardi lemba: Izi anena Iye wakukhala nayo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri: Ndidziwa ntchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo uli wakufa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Sardi lemba: Izi anena Iye wakukhala nayo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri: Ndidziwa ntchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo uli wakufa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 “Mtsogoleri wa mpingo wa ku Sardi umlembere kuti, Naŵa mau ochokera kwa amene amalamulira mizimu ya Mulungu isanu ndi iŵiri ija, ndi nyenyezi zisanu ndi ziŵiri zija zili m'manja mwakezi. Akuti: Ntchito zanu zonse ndikuzidziŵa. Ndikudziŵa kuti muli ndi mbiri yoti ndinu amoyo, chonsecho ndinu akufa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 “Lembera mngelo wampingo wa ku Sarde kuti: Awa ndi mawu ochokera kwa amene amasunga mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri. Iye akuti: Ndimadziwa ntchito zako; umadziwika kuti ndiwe wamoyo koma ndiwe wakufa. Onani mutuwo |