Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 22:2 - Buku Lopatulika

2 Pakati pa khwalala lake, ndi tsidya ili la mtsinje, ndi tsidya lake lija panali mtengo wa moyo wakubala zipatso khumi ndi ziwiri, ndi kupatsa zipatso zake mwezi ndi mwezi; ndipo masamba a mtengo ndiwo akuchiritsa nao amitundu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Pakati pa khwalala lake, ndi tsidya ili la mtsinje, ndi tsidya lake lija panali mtengo wa moyo wakubala zipatso khumi ndi ziwiri, ndi kupatsa zipatso zake mwezi ndi mwezi; ndipo masamba a mtengo ndiwo akuchiritsa nao amitundu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Unkayenda pakati pa mseu wamumzinda uja. Pa mbali zonse ziŵiri za mtsinje panali mtengo wopatsa moyo. Mtengowo umabala zipatso khumi ndi kaŵiri pa chaka, kamodzi mwezi uliwonse, ndipo masamba ake ndi ochiritsa anthu a mitundu yonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ukuyenda pakati pa msewu waukulu wa mu mzindawo. Mbali iliyonse ya mtsinjewo kunali mtengo wamoyo, utabala zipatso khumi ndi ziwiri. Kubereka zipatso mwezi uliwonse. Ndipo masamba a mtengowo ndi mankhwala wochiritsa anthu a mitundu ina.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 22:2
20 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova Mulungu anameretsa m'nthaka mitengo yonse yokoma m'maso ndi yabwino kudya; ndiponso mtengo wa moyo pakati pamundapo, ndi mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa.


Achiritsa osweka mtima, namanga mabala ao.


Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira; wakuiumirira ngwodala.


Nenepetsa mtima wa anthu awa, lemeretsa makutu ao, nutseke maso ao; angaone ndi maso ao, angamve ndi makutu ao, angazindikire ndi mtima wao, nakabwerenso, nachiritsidwe.


Mundichiritse ine, Yehova, ndipo ndidzachiritsidwa; mundipulumutse ine, ndipo ndidzapulumutsidwa; pakuti chilemekezo changa ndinu.


Ndipo anandibwezera ku khomo la nyumba, ndipo taonani, panatumphuka madzi pansi pa chiundo cha nyumba kum'mawa; pakuti khomo lake la nyumba linaloza kum'mawa; ndipo madzi anatsika kuchokera pansi pa nyumba, kumbali ya lamanja lake, kumwera kwa guwa la nsembe.


Ndidzachiritsa kubwerera kwao, ndidzawakonda mwaufulu; pakuti mkwiyo wanga wamchokera.


Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo kuti madzi amoyo adzatuluka ku Yerusalemu; gawo lao lina kunka ku nyanja ya kum'mawa, ndi gawo lina kunka ku nyanja ya kumadzulo; adzatero nyengo ya dzinja ndi ya mwamvu.


Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakutulukirani, muli kuchiritsa m'mapiko mwake; ndipo mudzatuluka ndi kutumphatumpha ngati anaang'ombe onenepa otuluka m'khola.


Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino: anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyanso, kutulutsa ndi ufulu ophwanyika,


amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.


Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye amene apambana ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli mu Paradaiso wa Mulungu.


Ndipo zitseko khumi ndi ziwiri ndizo ngale khumi ndi ziwiri; chitseko chilichonse pa chokha cha ngale imodzi. Ndipo khwalala la mzinda nla golide woyengeka, ngati mandala openyekera.


Ndipo amitundu adzayendayenda mwa kuunika kwake; ndi mafumu a dziko atenga ulemerero wao kulowa nao momwemo.


Ndipo anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo, wonyezimira ngati krustalo, otuluka kumpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa.


Odala iwo amene atsuka miinjiro yao, kuti akakhale nao ulamuliro pa mtengo wa moyo, ndi kuti akalowe m'mzinda pazipata.


ndipo aliyense akachotsako pa mau a buku la chinenero ichi, Mulungu adzamchotsera gawo lake pa mtengo wa moyo, ndi m'mzinda woyerawo, ndi pa izi zilembedwa m'bukumu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa