Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 2:18 - Buku Lopatulika

18 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Tiatira lemba: Izi azinena Mwana wa Mulungu, wakukhala nao maso ake ngati lawi la moto, ndi mapazi ake ngati mkuwa wonyezimira:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Tiatira lemba: Izi azinena Mwana wa Mulungu, wakukhala nao maso ake ngati lawi la moto, ndi mapazi ake ngati mkuwa wonyezimira:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 “Mtsogoleri wa mpingo wa ku Tiatira umlembere kuti: Naŵa mau ochokera kwa Mwana wa Mulungu, uja ali ndi maso onyezimira ngati malaŵi a moto, ndi mapazi onga chitsulo choŵala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 “Lembera mngelo wampingo wa ku Tiyatira kuti: Awa ndi mawu ochokera kwa Mwana wa Mulungu, amene maso ake ali ngati moto woyaka ndi mapazi ake ngati chitsulo chonyezimira.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 2:18
22 Mawu Ofanana  

Ndidzauza za chitsimikizo: Yehova ananena ndi Ine, Iwe ndiwe Mwana wanga; Ine lero ndakubala.


thupi lake lomwe linanga berulo, ndi nkhope yake ngati maonekedwe a mphezi, ndi maso ake ngati nyali zamoto, ndi manja ake ndi mapazi ake akunga mkuwa wonyezimira, ndi kumveka kwa mau ake kunanga phokoso la aunyinji.


Akali chilankhulire, onani, mtambo wowala unawaphimba iwo: ndipo onani, mau ali kunena mumtambo, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.


Ndipo anali naye akudikira Yesu, anaona chivomezi, ndi zinthu zimene zinachitidwa, anaopa kwambiri, nanena, Indedi Uyu ndiye Mwana wa Mulungu.


ndipo onani, mau akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.


Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: chifukwa chakenso Choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu.


Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.


Natanaele anayankha Iye, Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu mfumu ya Israele.


kodi inu munena za Iye, amene Atate anampatula namtuma kudziko lapansi, Uchita mwano; chifukwa ndinati, Ndili Mwana wa Mulungu?


Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.


Wokhulupirira Iye saweruzidwa; wosakhulupirira waweruzidwa ngakhale tsopano, chifukwa sanakhulupirire dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.


Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo ilipo tsopano, imene akufa adzamva mau a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo.


Ndipo anatimva mkazi wina dzina lake Lidia, wakugulitsa chibakuwa, wa kumzinda wa Tiatira, amene anapembedza Mulungu; mtima wake Ambuye anatsegula; kuti amvere zimene anazinena Paulo.


Ndipo monga anapita panjira pao, anadza kumadzi akuti; ndipo mdindoyo anati, Taonapo madzi; chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe?


amene anatsimikizidwa ndi mphamvu kuti ndiye Mwana wa Mulungu monga mwa Mzimu wa chiyero, ndi kuuka kwa akufa; ndiye Yesu Khristu Ambuye wathu;


Iye amene sanatimane Mwana wake wa Iye yekha, koma anampereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi Iye?


ndi kuti, Chimene upenya, lemba m'buku, nulitumize kwa Mipingo isanu ndi iwiri, ku Efeso, ndi ku Smirina, ndi ku Pergamo, ndi ku Tiatira, ndi ku Sardi, ndi ku Filadelfiya, ndi ku Laodikea.


Kwa mngelo wa Mpingo wa ku Efeso lemba: Izi azinena Iye amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziwiri m'dzanja lake lamanja, Iye amene ayenda pakati pa zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide:


Koma ndinena kwa inu, kwa otsala a ku Tiatira, onse amene alibe chiphunzitso ichi, amene sanazindikire zakuya za Satana, monga anena, Sindikusanjikizani katundu wina.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa