Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 2:16 - Buku Lopatulika

16 Chifukwa chake lapa; ukapanda kutero ndidza kwa iwe posachedwa, ndipo ndidzachita nao nkhondo ndi lupanga la m'kamwa mwanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Chifukwa chake lapa; ukapanda kutero ndidza kwa iwe posachedwa, ndipo ndidzachita nao nkhondo ndi lupanga la m'kamwa mwanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Mutembenuke mtima tsono. Mukapanda kutero, ndidzabwera kwanuko posachedwa, ndipo ndidzakuthirani nkhondo ndi lupanga lotulukira m'kamwa mwanga lija.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Tsono tembenukani mtima. Mukapanda kutero, ndidzabwera kwanuko posachedwa ndipo ndidzachita nanu nkhondo ndi lupanga lotuluka mʼkamwa mwanga lija.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 2:16
15 Mawu Ofanana  

koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m'dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yake.


nachititsa pakamwa panga ngati lupanga lakuthwa, mu mthunzi wa dzanja lake wandibisa Ine; wandipanga Ine; muvi wotuulidwa; m'phodo mwake Iye wandisungitsa Ine, nati kwa Ine,


Mutengenso chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu;


Ndipo pamenepo adzavumbulutsidwa wosaweruzikayo, amene Ambuye Yesu adzamthera ndi mzimu wa pakamwa pake, nadzamuononga ndi maonekedwe a kudza kwake;


Ndipo m'dzanja lake lamanja munali nyenyezi zisanu ndi ziwiri; ndi m'kamwa mwake mudatuluka lupanga lakuthwa konsekonse; ndipo nkhope yake ngati dzuwa lowala mu mphamvu yake.


Ndipo anatenthedwa anthu ndi kutentha kwakukulu; ndipo anachitira mwano dzina la Mulungu wokhala nao ulamuliro pa miliri iyi; ndipo sanalape kuti amchitire ulemu.


Ndipo m'kamwa mwake mutuluka lupanga lakuthwa, kuti akanthe nalo mitundu ya anthu; ndipo Iye adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo: ndipo aponda Iye moponderamo mphesa mwa vinyo waukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse.


ndipo otsalawa anaphedwa ndi lupanga la Iye wakukwera pa kavalo, ndilo lotuluka m'kamwa mwake; ndipo mbalame zonse zinakhuta ndi nyama zao.


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Pergamo lemba: Izi anena Iye wokhala nalo lupanga lakuthwa konsekonse:


Potero kumbukira kumene wagwerako, nulape, nuchite ntchito zoyamba; koma ngati sutero, ndidzadza kwa iwe, ndipo ndidzatunsa choikaponyali chako, kuchichotsa pamalo pake, ngati sulapa.


Iye wakuchitira umboni izi, anena, Indetu; ndidza msanga. Amen; idzani, Ambuye Yesu.


Ndipo taonani, ndidza msanga. Wodala iye amene asunga mau a chinenero cha buku ili.


Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa