Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 19:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo anagwa pansi akuluwo makumi awiri mphambu anai ndi zamoyo zinai, ndipo zinalambira Mulungu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kunena, Amen; Aleluya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo anagwa pansi akuluwo makumi awiri mphambu anai ndi zamoyo zinai, ndipo zinalambira Mulungu wakukhala pa mpando wachifumu, nizinena, Amen; Aleluya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Akuluakulu 24 aja, pamodzi ndi Zamoyo zinai zija, adadzigwetsa pansi moŵerama, napembedza Mulungu amene amakhala pa mpando wachifumu. Adayankha kuti, “Amen, Aleluya!”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Akuluakulu 24 aja ndi zamoyo zinayi zija anadzigwetsa pansi kupembedza Mulungu amene anakhala pa mpando waufumu. Ndipo anafuwula kuti, “Ameni, Haleluya!”

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 19:4
20 Mawu Ofanana  

Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele, kuyambira kosayamba kufikira kosatha. Ndipo anthu onse anati, Amen! Nalemekeza Yehova.


Ndinakutumulanso malaya anga, ndi kuti, Mulungu akutumule momwemo munthu yense wosasunga mau awa, kunyumba yake, ndi kuntchito yake; inde amkutumule momwemo, namtayire zake zonse. Ndi msonkhano wonse unati, Amen, nalemekeza Yehova. Ndipo anthu anachita monga mwa mau awa.


Pamenepo Ezara analemekeza Yehova Mulungu wamkulu. Navomereza anthu onse, ndi kuti, Amen, Amen; nakweza manja ao, nawerama, nalambira Yehova nkhope zao pansi.


Ochimwa athedwe kudziko lapansi, ndi oipa asakhalenso. Yamika Yehova, moyo wanga. Aleluya.


Wodala Yehova, Mulungu wa Israele, kuyambira kosayamba kufikira kosatha. Ndi anthu onse anene, Amen. Aleluya.


Wodalitsika Yehova, Mulungu wa Israele, kuchokera nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha. Amen, ndi Amen.


Ndipo dzina lake la ulemerero lidalitsike kosatha; ndipo dziko lonse lapansi lidzale nao ulemerero wake. Amen, ndi Amen.


Wodalitsika Yehova kunthawi yonse. Amen ndi Amen.


Yeremiya mneneri anati, Amen: Yehova achite chotero: Yehova atsimikize mau ako amene wanenera, abwezerenso zipangizo za nyumba ya Yehova, ndi onse amene anachotsedwa am'nsinga, kuchokera ku Babiloni kudza kumalo kuno.


ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.


Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.


Chifukwa ngati udalitsa ndi mzimu, nanga iye wakukhala wosaphunzira adzati Amen bwanji, pa kuyamika kwako, popeza sadziwa chimene unena?


Ndipo chimodzi cha zamoyo zinai chinapatsa angelo asanu ndi awiri mbale zisanu ndi ziwiri zagolide zodzala ndi mkwiyo wa Mulungu wakukhala ndi moyo ku nthawi za nthawi.


Zitatha izi ndinamva ngati mau aakulu a khamu lalikulu mu Mwamba, lili kunena, Aleluya; chipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu, nza Mulungu wathu;


Ndipo anatinso, Aleluya. Ndipo utsi wake ukwera kunthawi za nthawi.


Ndipo ndinamva ngati mau a khamu lalikulu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mau a mabingu olimba, ndi kunena, Aleluya; pakuti achita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse.


Ndipo zamoyo zinai zinati, Amen. Ndipo akuluwo anagwa pansi nalambira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa