Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 18:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo ochita malonda a m'dziko adzalira nadzauchitira chifundo, popeza palibe munthu agulanso malonda ao;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo ochita malonda a m'dziko adzalira nadzauchitira chifundo, popeza palibe munthu agulanso malonda ao;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Anthu amalonda a pa dziko lapansi adzalira ndi kumva naye chisoni kwambiri, pakuti palibenso wogula malonda ao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 “Amalonda a dziko lapansi adzalira nakhuza maliro ake chifukwa palibenso amene akugula katundu wawo,

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 18:11
18 Mawu Ofanana  

pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golide woyengeka.


Ndipo Babiloni, ulemerero wa maufumu, mudzi wokongolawo Ababiloni anaunyadira, adzakhala monga momwe Mulungu anapasula Sodomu ndi Gomora.


Zinthu zomwe unagwira ntchito yake, zidzatero nawe; iwo amene anachita malonda ndi iwe chiyambire pa ubwana wako, adzayenda yense kunka kumalo kwake; sipadzakhala wopulumutsa iwe.


Akulu a ku Gebala ndi eni luso ake anali mwa iwe kukonza ziboo zako; zombo zonse za kunyanja pamodzi ndi amalinyero ao anali mwa iwe kusinthana nawe malonda.


Chemani okhala m'chigwa, pakuti amalonda onse atayika, onsewo osenza siliva aonongeka.


Ngakhale siliva wao, ngakhale golide wao sizidzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova; koma dziko lonse lidzatha ndi moto wa nsanje yake; pakuti adzachita chakutsiriza, mofulumira, onse okhala m'dziko.


Koma iwo ananyalanyaza, nachoka, wina kumunda wake, wina kumalonda ake:


nati kwa iwo akugulitsa nkhunda, Chotsani izi muno; musamayesa nyumba ya Atate wanga nyumba ya malonda.


Ndipo m'chisiriro adzakuyesani malonda ndi mau onyenga; amene chiweruzo chao sichinachedwe ndi kale lomwe, ndipo chitayiko chao sichiodzera.


Otsatsa izi, olemezedwa nao, adzaima patali chifukwa cha kuopa chizunzo chake, nadzalira, ndi kuchita chifundo;


Kondwera pa iye, m'mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndi atumwi, ndi aneneri inu; chifukwa Mulungu anauweruzira kuweruzidwa kwanu.


ndi kuunika kwa nyali sikudzaunikiranso konse mwa iwe; ndi mau a mkwati ndi a mkwatibwi sadzamvekanso konse mwa iwe; pakuti otsatsa malonda anu anali omveka a m'dziko; pakuti ndi nyanga yako mitundu yonse inasokeretsedwa.


Chifukwa ndi vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake mitundu yonse idagwa; ndipo mafumu a dziko anachita naye chigololo; ndipo ochita malonda a dziko analemera ndi mphamvu ya kudyerera kwake.


Ndipo mafumu a dziko ochita chigololo nadyerera naye, adzalira nadzaulira maliro pamene aona utsi wa kutentha kwake, poima patali,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa