Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 16:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo wachiwiri anatsanulira mbale yake m'nyanja; ndipo kunakhala mwazi ngati wa munthu wakufa; ndipo zamoyo zonse za m'nyanja zidafa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo wachiwiri anatsanulira mbale yake m'nyanja; ndipo kunakhala mwazi ngati wa munthu wakufa; ndipo zamoyo zonse za m'nyanja zidafa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Pambuyo pake mngelo wachiŵiri adakhuthulira za mumkhate mwake pa nyanja. Pomwepo madzi ake adasanduka magazi, magazi ake ngati a munthu wakufa. Ndipo zamoyo zonse za m'nyanjamo zidafa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Mngelo wachiwiri anapita natsanula mbale yake pa nyanja ndipo madzi ake anasanduka magazi, magazi ake ngati a munthu wakufa. Chamoyo chilichonse cha mʼnyanjamo chinafa.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 16:3
10 Mawu Ofanana  

zonse zimene m'mphuno zao munali mpweya wa mzimu wa moyo, zonse zinali pamtunda, zinafa.


Anasanduliza madzi ao akhale mwazi, naphanso nsomba zao.


Nasanduliza nyanja yao mwazi, ndi mitsinje yao, kuti sangakhoze kumwa.


Ndipo ndidzaweruza mlandu wako, monga aweruza akazi achigololo ndi okhetsa mwazi; ndipo ndidzakutengera mwazi wa ukali ndi wa nsanje.


Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu.


ndipo anali nako m'dzanja lake kabuku kofunyulula: ndipo anaponda nalo phazi lake lamanja panyanja, ndi lamanzerelo pamtunda,


Izo zili nao ulamuliro wakutseka m'mwamba, isagwe mvula masiku a chinenero chao; ndipo ulamuliro zili nao pamadzi kuwasandutsa mwazi, ndi kupanda dziko ndi mliri uliwonse nthawi iliyonse zikafuna.


Ndipo ndinaimirira pa mchenga wa nyanja. Ndipo ndinaona chilombo chilinkutuluka m'nyanja, chakukhala nazo nyanga khumi, ndi mitu isanu ndi iwiri, ndi pa nyanga zake nduwira zachifumu khumi, ndi pamitu pake maina a mwano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa