Chivumbulutso 16:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera ku Kachisi, akunena kwa angelo asanu ndi awiri, Mukani, ndipo tsanulirani kudziko mbale zisanu ndi ziwiri za mkwiyo wa Mulungu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo ndinamva mau akulu ochokera ku Kachisi, akunena kwa angelo asanu ndi awiri, Mukani, ndipo tsanulirani kudziko mbale zisanu ndi ziwiri za mkwiyo wa Mulungu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Pambuyo pake ndidamva mau amphamvu ochokera m'Malo Opatulika aja. Adauza angelo asanu ndi aŵiri aja kuti, “Pitani, kathireni pa dziko lapansi ukali wa Mulungu, umene uli m'mikhate isanu ndi iŵiri ija.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Kenaka ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Nyumba ya Mulungu ija kuwuza angelo asanu ndi awiri kuti, “Pitani, katsanulireni pa dziko lapansi ukali wa Mulungu umene uli mʼmbale zisanu ndi ziwirizi!” Onani mutuwo |