Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 15:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo aimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo aimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ankaimba nyimbo ya Mose, mtumiki wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa uja. Mau ake ankati, “Ambuye, Mulungu Mphambe, ntchito zanu nzazikulu ndi zododometsa. Inu, Mfumu ya anthu a mitundu yonse, njira zanu nzolungama ndi zoona.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Iwo ankayimba nyimbo ya Mose, mtumiki wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwana Wankhosa. Nyimbo yake inkati, “Zochita zanu ndi zazikulu ndi zodabwitsa, Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse Njira zanu ndi zachilungamo ndi zoona, Mfumu ya mitundu yonse.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 15:3
49 Mawu Ofanana  

Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro.


Koma Aroni ndi ana ake ankafukiza paguwa la nsembe yopsereza, ndi paguwa la nsembe yofukiza, chifukwa cha ntchito yonse ya malo opatulika kwambiri, ndi kuchitira Israele chowatetezera, monga mwa zonse Mose mtumiki wa Mulungu adawauza.


Ndipo mfumu inaitana Yehoyada mkulu wao, niti naye, Unalekeranji kuuza Alevi abwere nao kuchokera mu Yuda ndi Yerusalemu msonkho wa Mose mtumiki wa Yehova, ndi wa msonkhano wa Israele, ukhale wa chihema cha umboni?


ndi Sabata lanu lopatulika munawadziwitsa, nimunawalamulira malamulo, ndi malemba, ndi chilamulo, mwa dzanja la Mose mtumiki wanu;


Kumbukirani kuti mukuze ntchito zake zimene anaziimbira anthu.


amene achita zazikulu ndi zosalondoleka, zinthu zodabwitsa zosawerengeka.


Pakuti Yehova ndiye wabwino; chifundo chake chimanka muyaya; ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo.


Kumbukirani zodabwitsa zake adazichita; zizindikiro zake ndi maweruzo a pakamwa pake;


Ntchito za Yehova nzazikulu, zofunika ndi onse akukondwera nazo.


Ntchito za manja ake ndizo choonadi ndi chiweruzo; malangizo ake onse ndiwo okhulupirika.


Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.


Yehova ali wolungama m'njira zake zonse, ndi wachifundo m'ntchito zake zonse.


Ndipo adzanenera mphamvu za ntchito zanu zoopsa; ndi ukulu wanu ndidzaufotokozera.


Mulungu ndiye wangwiro m'njira zake; mau a Yehova ngoyengeka; ndiye chikopa cha onse okhulupirira Iye.


Anachita chodabwitsa pamaso pa makolo ao, m'dziko la Ejipito kuchidikha cha Zowani.


Ha! Ntchito zanu nzazikulu, Yehova, zolingalira zanu nzozama ndithu.


Ndipo mphamvu ya mfumu ikonda chiweruzo; Inu mukhazikitsa zolunjika, muchita chiweruzo ndi chilungamo mu Yakobo.


Pakuti Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu; Iye adzatipulumutsa.


Nenani inu, tulutsani mlandu wanu; inde, achite uphungu pamodzi; ndani waonetsa ichi chiyambire nthawi yakale? Ndani wanena ichi kale? Kodi si ndine Yehova? Ndipo palibenso Mulungu wina popanda Ine; Mulungu wolungama, ndi Mpulumutsi; palibenso wina popanda Ine.


Ndipo poyandikira padzenje inafuula ndi mau achisoni mfumu, ninena, niti kwa Daniele, Daniele, mnyamata wa Mulungu wamoyo, kodi Mulungu wako, amene umtumikira kosalekeza, wakhoza kukulanditsa kwa mikango?


Inde Israele yense walakwira chilamulo chanu, ndi kupatuka, kuti asamvere mau anu; chifukwa chake temberero lathiridwa pa ife, ndi lumbiro lolembedwa m'chilamulo cha Mose mtumiki wa Mulungu; pakuti tamchimwira.


Wanzeru ndani, kuti azindikire izi? Waluntha, kuti adziwe izi? Pakuti njira za Yehova zili zoongoka; ndipo olungama adzayendamo, koma olakwa adzagwamo.


Mudzapatsa kwa Yakobo choonadi, ndi kwa Abrahamu chifundo chimene munalumbirira makolo athu kuyambira masiku a kale lomwe.


Yehova pakati pake ali wolungama; sadzachita chosalungama, m'mawa ndi m'mawa aonetsera chiweruzo chake poyera, chosasowa kanthu; koma wosalungama sadziwa manyazi.


Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.


Chifukwa chilamulo chinapatsidwa mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinadza mwa Yesu Khristu.


Ndipo Mose ananena mau a nyimbo iyi m'makutu mwa msonkhano wonse wa Israele, kufikira adatha.


Pakuti ndidzalalika dzina la Yehova. Nenani kuti Mulungu wathu ndi wamkulu.


Ndipo Mose mtumiki wa Yehova anamwalirako m'dziko la Mowabu, monga mwa mau a Yehova.


Ndipo kwa Mfumu yosatha, yosavunda, yosaoneka, Mulungu wa yekha, ukhale ulemu ndi ulemerero, kufikira nthawi za nthawi. Amen.


Ndipo Mosetu anali wokhulupirika m'nyumba yake yonse, monga mnyamata, achitire umboni izi zidzalankhulidwazi;


Koma samalirani bwino kuti muchite chilangizo ndi chilamulo zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zake zonse ndi kusunga malamulo ake, ndi kumuumirira Iye, ndi kumtumikira Iye ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.


Ine ndine Alefa ndi Omega, ati Ambuye Mulungu, amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse.


nati, Tikuyamikani, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, amene muli, nimunali; popeza mwadzitengera mphamvu yanu yaikulu, ndipo mwachita ufumu.


ndipo aimba ngati nyimbo yatsopano kumpando wachifumu, ndi pamaso pa zamoyo zinai, ndi akulu; ndipo palibe munthu anakhoza kuphunzira nyimboyi, koma zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, ogulidwa kuchokera kudziko.


Ndipo anatsata mngelo wina mnzake ndi kunena, Wagwa, wagwa, Babiloni waukulu umene unamwetsako mitundu yonse ku vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake.


Iwo adzachita nkhondo pa Mwanawankhosa, ndipo Mwanawankhosa adzawagonjetsa, chifukwa ali Mbuye wa ambuye, ndi Mfumu ya mafumu; ndipo adzawalakanso iwo akukhala naye, oitanidwa, ndi osankhika ndi okhulupirika.


Ndipo ali nalo pa chovala chake ndi pa ntchafu yake dzina lolembedwa, MFUMU YA MAFUMU, NDI MBUYE WA AMBUYE.


pakuti maweruzo ake ali oona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene anaipsa dziko ndi chigololo chake, ndipo anabwezera chilango mwazi wa akapolo ake padzanja lake la mkaziyo.


Ndipo zamoyozo zinai, chonse pa chokha chinali nao mapiko asanu ndi limodzi; ndipo zinadzala ndi maso pozinga ponse ndi m'katimo; ndipo sizipumula usana ndi usiku, ndi kunena, Woyera, woyera, woyera, Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, amene anali, amene ali, ndi amene alinkudza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa