Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 15:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo ndinaona ngati nyanja yagalasi yosakaniza ndi moto; ndipo iwo amene anachigonjetsa chilombocho, ndi fano lake ndi chiwerengero cha dzina lake, anaimirira pa nyanja yagalasi, nakhala nao azeze a Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo ndinaona ngati nyanja yagalasi yosanganiza ndi moto; ndipo iwo amene anachilaka chilombocho, ndi fano lake ndi chiwerengero cha dzina lake, anaimirira pa nyanja yagalasi, nakhala nao azeze a Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Kenaka ndidaona ngati nyanja ya galasi losanganiza ndi moto. Ndidaonanso anthu amene adapambana chilombo chija, fano lake lija, ndi nambala yotanthauza dzina lake. Anthuwo adaaimirira pamphepete pa nyanja yagalasi ija, m'manjamu ali ndi azeze oŵapatsa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ndipo ndinaona chimene chinaoneka ngati nyanja yonyezimira yosakaniza ndi moto, ndipo pambali pa nyanjayo panayima amene anagonjetsa chirombo chija ndi fano lake, ndi nambala yotanthauza dzina lake. Anthuwo ananyamula azeze amene Mulungu anawapatsa.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 15:2
14 Mawu Ofanana  

Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:


kuti mayesedwe a chikhulupiriro chanu, ndiwo a mtengo wake woposa wa golide amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe ochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa vumbulutso la Yesu Khristu;


Okondedwa, musazizwe ndi mayesedwe amoto adakugwerani inu akhale chakukuyesani, ngati chinthu chachilendo chachitika nanu:


Ndipo iwo anampambana iye chifukwa cha mwazi wa Mwanawankhosa, ndi chifukwa cha mau a umboni wao; ndipo sanakonde moyo wao kungakhale kufikira imfa.


Ndipo ndinaimirira pa mchenga wa nyanja. Ndipo ndinaona chilombo chilinkutuluka m'nyanja, chakukhala nazo nyanga khumi, ndi mitu isanu ndi iwiri, ndi pa nyanga zake nduwira zachifumu khumi, ndi pamitu pake maina a mwano.


Ndipo chisokeretsa iwo akukhala padziko ndi zizindikiro zimene anachipatsa mphamvu yakuzichita pamaso pa chilombo, ndi kunena kwa iwo akukhala padziko, kuti apange fano la chilombocho, chimene chinali nalo bala la lupanga ndi kukhalanso ndi moyo.


ndi kuti munthu sangakhoze kugula kapena kugulitsa, koma iye yekha wakukhala nacho chilembo, ndilo dzina la chilombo, kapena chiwerengero cha dzina lake.


Ndipo mirimo ya linga lake ndi yaspi; ndipo mzindawo ngwa golide woyengeka, wofanana ndi mandala oyera.


ndipo kumpandowo, ngati nyanja yagalasi yonga krustalo; ndipo pakati pa mpandowo, ndi pozinga mpandowo, zamoyo zinai zodzala ndi maso kutsogolo ndi kumbuyo.


Ndipo pamene adatenga bukulo, zamoyo zinai ndi akulu makumi awiri mphambu anai zinagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosa, zonse zili nao azeze, ndi mbale zagolide zodzala ndi zofukiza, ndizo mapemphero a oyera mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa