Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 15:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo ndinaona chizindikiro china m'mwamba, chachikulu ndi chozizwitsa, angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, ndiyo yotsiriza, kuti mwa iyo watsirizika mkwiyo wa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo ndinaona chizindikiro china m'mwamba, chachikulu ndi chozizwitsa, angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, ndiyo yotsiriza, kuti mwa iyo watsirizika mkwiyo wa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pambuyo pake ndidaona Kumwamba chizindikiro china chachikulu ndi chododometsa: angelo asanu ndi aŵiri okhala ndi miliri isanu ndi iŵiri. Miliriyo ndi yotsiriza, pakuti ukali wa Mulungu uthera pa imeneyi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Kumwamba ndinaona chizindikiro china chachikulu ndi chodabwitsa: angelo asanu ndi awiri ali ndi miliri isanu ndi iwiri yomaliza chifukwa Mulungu anakwiya kotheratu.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 15:1
21 Mawu Ofanana  

Iye apulumutsa, nalanditsa, nachita zizindikiro ndi zozizwa m'mwamba ndi padziko lapansi, ndiye amene anapulumutsa Daniele kumphamvu ya mikango.


Ndipo mukayenda motsutsana nane, osalola kumvera Ine; ndidzakuonjezerani miliri kasanu ndi kawiri, monga mwa zochimwa zanu.


nafuula ndi mau aakulu, monga ngati mkango ubangula; ndipo pamene anafuula mabingu asanu ndi awiri analankhula mau ao.


Tsoka lachiwiri lachoka; taonani, tsoka lachitatu lidza msanga.


iyenso adzamwako kuvinyo wa mkwiyo wa Mulungu, wokonzeka wosasakaniza m'chikho cha mkwiyo wake; ndipo adzazunzika ndi moto ndi sulufure pamaso pa angelo oyera mtima ndi pamaso pa Mwanawankhosa;


Ndipo mngelo anaponya chisenga chake kudziko nadula mphesa za m'munda wa m'dziko, naziponya moponderamo mphesa mwamukulu mwa mkwiyo wa Mulungu.


Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera ku Kachisi, akunena kwa angelo asanu ndi awiri, Mukani, ndipo tsanulirani kudziko mbale zisanu ndi ziwiri za mkwiyo wa Mulungu.


Ndipo anadza mmodzi mwa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, nalankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa chitsutso cha mkazi wachigololo wamkulu, wakukhala pamadzi ambiri,


Ndipo m'kamwa mwake mutuluka lupanga lakuthwa, kuti akanthe nalo mitundu ya anthu; ndipo Iye adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo: ndipo aponda Iye moponderamo mphesa mwa vinyo waukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse.


Ndipo anadza mmodzi wa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, zodzala ndi miliri yotsiriza isanu ndi iwiri; ndipo analankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.


Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva chiombankhanga chilikuuluka pakati pamwamba, ndi kunena ndi mau aakulu, Tsoka, tsoka, tsoka, iwo akukhala padziko, chifukwa cha mau otsala a lipenga la angelo atatu asanaombe.


Ndipo ndinaona angelo asanu ndi awiri amene amaimirira pamaso pa Mulungu; ndipo anawapatsa malipenga asanu ndi awiri.


Ndipo angelo asanu ndi awiri akukhala nao malipenga anadzikonzera kuti aombe.


Ndipo otsala a anthu osaphedwa nayo miliri iyo sanalape ntchito ya manja ao, kuti asapembedzere ziwanda, ndi mafano agolide, ndi asiliva, ndi amkuwa, ndi a mwala, ndi amtengo, amene sangathe kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa