Chivumbulutso 13:12 - Buku Lopatulika12 Ndipo chichita ulamuliro wonse wa chilombo choyamba pamaso pake. Ndipo chilambiritsa dziko ndi iwo akukhala momwemo chilombo choyamba, chimene bala lake la kuimfa lidapola. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Ndipo chichita ulamuliro wonse wa chilombo choyamba pamaso pake. Ndipo chilambiritsa dziko ndi iwo akukhala momwemo chilombo choyamba, chimene bala lake la kuimfa lidapola. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Chinkalamulira pamaso pa chilombo choyamba chija ndi mphamvu zimene chilombo choyambacho chidaachipatsa. Chinkakakamiza dziko lapansi ndi onse okhalamo kuti azipembedza chilombo choyamba chija chimene bala lake lofa nalo lija linali litapola. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Chinalamulira ndi mphamvu zonse za chirombo choyamba chija, ndipo chinachititsa kuti dziko lapansi ndi anthu okhalamo alambire chirombo choyamba chija, chimene bala lake losati nʼkupola linali litapola. Onani mutuwo |
Chilombo chimene unachiona chinaliko, koma kulibe; ndipo chidzatuluka m'chiphompho chakuya, ndi kunka kuchitayiko. Ndipo adzazizwa iwo akukhala padziko amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo chiyambire makhazikidwe a dziko lapansi, pakuona chilombo, kuti chinaliko, ndipo kulibe, ndipo chidzakhalako.
Ndipo ndinaona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambire chilombo, kapena fano lake, nisanalandire lembalo pamphumi ndi padzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Khristu zaka chikwi.