Chivumbulutso 12:4 - Buku Lopatulika4 Ndipo mchira wake uguza limodzi la magawo atatu a nyenyezi zam'mwamba, nuziponya padziko. Ndipo chinjoka chinaimirira pamaso pa mkazi akuti abale, kuti, akabala icho chikalikwire mwana wake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Ndipo mchira wake uguza limodzi la magawo atatu a nyenyezi zam'mwamba, nuziponya padziko. Ndipo chinjoka chinaimirira pamaso pa mkazi akuti abale, kuti, akabala icho chikalikwire mwana wake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Ndi mchira wake chidakokolola chimodzi mwa zigawo zitatu za nyenyezi zakuthambo, nkuzigwetsa pa dziko lapansi. Chinjokacho chidadzaimirira pamaso pa mai uja amene anali pafupi kubala mwana, kuti akangobadwa mwanayo, chimudye. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Mchira wake unakokolola gawo limodzi la magawo atatu a nyenyezi kuzichotsa ku thambo ndi kuziponya pa dziko lapansi. Chinjoka chija chinadzayima patsogolo pa mayi uja amene anali pafupi kuberekayu kuti mwanayo akangobadwa chimudye. Onani mutuwo |