Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 11:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo pamene zidatsiriza umboni wao chilombo chokwera kutuluka m'chiphompho chakuya chidzachita nazo nkhondo, ndipo chidzazigonjetsa, ndi kupha izo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo pamene zidatsiriza umboni wao chilombo chokwera kutuluka m'chiphompho chakuya chidzachita nazo nkhondo, nichidzazilaka, nichidzazipha izo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Tsono mbonizo zikadzatsiriza umboni waowo, chilombo chotuluka m'Chiphompho chija chidzachita nazo nkhondo. Chidzazigonjetsa nkuzipha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Tsono zikadzatsiriza umboni wawowo, chirombo chotuluka mʼChidzenje chakuya chija chidzachita nawo nkhondo nʼkuzigonjetsa mpaka kuzipha.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 11:7
20 Mawu Ofanana  

Nidzanena mau akutsutsana ndi Wam'mwambamwamba, nidzalemetsa opatulika a Wam'mwambamwamba, nidzayesa kusintha nthawizo ndi chilamulo; ndipo adzaperekedwa m'dzanja lake mpaka nthawi imodzi, ndi nthawi zina, ndi nthawi yanusu.


Ndipo Iye anati kwa iwo, Pitani kauzeni nkhandweyo, Taonani, nditulutsa ziwanda, nditsiriza machiritso lero ndi mawa, ndipo mkucha nditsirizidwa.


Ndipo zinampempha Iye, kuti asazilamulire zichoke kulowa ku chiphompho chakuya.


Ine ndalemekeza Inu padziko lapansi, m'mene ndinatsiriza ntchito imene munandipatsa ndichite.


Pamene Yesu tsono adalandira vinyo wosasayo anati, Kwatha; ndipo anawerama mutu, napereka mzimu.


Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.


Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga chikhulupiriro:


Ndipo ndidzalamulira mboni zanga ziwiri, ndipo zidzanenera masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri amphambu makumi asanu ndi limodzi, zovala chiguduli.


Ndipo chinjoka chinakwiya ndi mkazi, ndipo chinachoka kunka kuchita nkhondo ndi otsala a mbeu yake, amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nao umboni wa Yesu.


Ndipo ndinaona chilombo china chilikutuluka pansi; ndipo chinali nazo nyanga ziwiri ngati za mwanawankhosa, ndipo chinalankhula ngati chinjoka.


Ndipo anachipatsa icho kuchita nkhondo ndi oyera mtima, ndi kuwagonjetsa; ndipo anachipatsa ulamuliro wa pa fuko lililonse, ndi anthu, ndi manenedwe, ndi mitundu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa