Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 11:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo anamva mau aakulu akuchokera Kumwamba akunena nao, Kwerani kuno. Ndipo anakwera kunka Kumwamba mumtambo; ndipo adani ao anawapenya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo anamva mau akulu akuchokera Kumwamba akunena nao, Kwerani kuno. Ndipo anakwera kunka Kumwamba mumtambo; ndipo adani ao anawapenya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Aneneri aja adamva mau amphamvu ochokera Kumwamba oŵauza kuti, “Bwerani kuno.” Iwowo adapitadi Kumwamba mu mtambo, adani ao aja akuŵapenya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Kenaka aneneri aja anamva mawu ofuwula ochokera kumwamba owawuza kuti, “Bwerani kuno.” Ndipo anapitadi kumwamba mu mtambo adani awo aja akuwaona.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 11:12
21 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, pamene Yehova adati akweze Eliya kumwamba ndi kamvulumvulu, Eliya anachokera ku Giligala pamodzi ndi Elisa.


Ndipo kunachitika, akali chiyendere ndi kukambirana, taonani, anaoneka galeta wamoto ndi akavalo amoto, nawalekanitsa awiriwa; Eliya nakwera kumwamba ndi kamvulumvulu.


Pamenepo ana a aneneri okhala ku Yeriko anayandikira kwa Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akuchotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati iye, Inde ndidziwa, khalani muli chete.


Ndipo anthu makumi asanu a ana a aneneri anapita, naima patali pandunji pao, iwo awiri naima ku Yordani.


Woipa adzaziona, nadzapsa mtima; adzakukuta mano, nadzasungunuka; chokhumba oipa chidzatayika.


Yehova, ndani adzagonera m'chihema mwanu? Adzagonera ndani m'phiri lanu lopatulika?


Adzakwera ndani m'phiri la Yehova? Nadzaima m'malo ake oyera ndani?


Mundichitire chizindikiro choti chabwino; kuti ondida achione, nachite manyazi, popeza Inu, Yehova, munandithandiza ndi kundisangalatsa.


Ndipo anagulula njinga za magaleta ao, nawayendetsa molemetsa; pamenepo Aejipito anati, Tithawe pamaso pa Israele; pakuti Yehova alikuwagwirira nkhondo pa Aejipito.


Ndipo iwe unati mumtima mwako, Ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wachifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pamwamba paphiri la khamu, m'malekezero a kumpoto;


koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.


Ndani awa amene auluka ngati mtambo, ndi monga nkhunda kumazenera ao?


Pamenepo mudzabwera ndi kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosamtumikira.


Ndipo m'dziko la akufa anakweza maso ake, pokhala nao mazunzo, naona Abrahamu patali, ndi Lazaro m'chifuwa mwake.


Ndipo m'mene adanena izi, ali chipenyerere iwo, ananyamulidwa; ndipo mtambo unamlandira Iye kumchotsa kumaso kwao.


pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nao pamodzi m'mitambo, kukakomana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse.


Ndipo anabala mwana wamwamuna, amene adzaweruza mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo: ndipo anakwatulidwa mwana wake amuke kwa Mulungu, ndi kumpando wachifumu wake.


Iye wakupambana, ndidzampatsa akhale pansi ndi Ine pa mpando wachifumu wanga, monga Inenso ndinapambana, ndipo ndinakhala pansi ndi Atate wanga pa mpando wachifumu wake.


Zitatha izi ndinapenya, ndipo taonani, khomo lotseguka mu Mwamba, ndipo mau oyamba ndinawamva, ngati lipenga lakulankhula ndi ine, anati, Kwera kuno, ndipo ndidzakuonetsa zimene ziyenera kuchitika m'tsogolomo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa