Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 10:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo ndinamuka kwa mngelo, ndi kunena naye, Ndipatse kabukuko. Ndipo ananena ndi ine, Dzatenge, nudye; ndipo kadzawawitsa m'mimba mwako, komatu m'kamwa mwako kadzazuna ngati uchi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo ndinamuka kwa mngelo, ndi kunena naye, Ndipatse kabukuko. Ndipo ananena ndi ine, Dzatenge, nudye; ndipo kadzawawitsa m'mimba mwako, komatu m'kamwa mwako kadzazuna ngati uchi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ndidapitadi kwa mngeloyo nkumupempha kuti andipatse kampukutuko. Iye adati, “Kwaya, idya. M'mimba mwako kaziŵaŵa, koma m'kamwa mwako kazizuna ngati uchi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Choncho ndinapita kwa mngeloyo ndipo ndinamupempha kuti andipatse kabukuko. Iye anati, “Tenga, idya. Mʼmimba mwako kaziwawa koma mʼkamwa mwako kazizuna ngati uchi.”

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 10:9
7 Mawu Ofanana  

Sindinabwerera kusiya malamulo a pa milomo yake; ndasungitsa mau a pakamwa pake koposa lamulo langalanga.


Mau anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mau anu anakhala kwa ine chikondwero ndi chisangalalo cha mtima wanga; pakuti ndatchedwa dzina lanu, Yehova Mulungu wa makamu.


Koma iwe, wobadwa ndi munthu, tamvera ichi ndilikunena nawe; usakhale iwe wopanduka, ngati nyumba ija yopanduka; tsegula pakamwa pako, nudye chomwe ndikupatsa.


M'mwemo mzimu unandinyamula ndi kuchoka nane; ndipo ndinamuka wowawidwa, womyuka mtima; koma dzanja la Yehova linandigwirizitsa.


chifukwa cha izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera;


Ndipo ndinatenga kabuku m'dzanja la mngelo, ndipo ndinakadya; ndipo kanali m'kamwa mwanga kozuna ngati uchi; ndipo pamene ndinakadya m'mimba mwanga mudawawa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa