Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 10:7 - Buku Lopatulika

7 komatu m'masiku a mau a mngelo wachisanu ndi chiwiri m'mene iye adzayamba kuomba lipenga, pamenepo padzatsirizika chinsinsi cha Mulungu, monga analalikira kwa akapolo ake aneneri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 komatu m'masiku a mau a mngelo wachisanu ndi chiwiri m'mene iye adzayamba kuomba lipenga, pamenepo padzatsirizika chinsinsi cha Mulungu, monga analalikira kwa akapolo ake aneneri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Pamene mngelo wachisanu ndi chiŵiri adzaliza lipenga lake, zachinsinsi zimene Mulungu adakonzeratu zidzachitika, monga momwe Iye adaalonjezera kwa atumiki ake aja, aneneri.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Koma patsala pangʼono kuti mngelo wachisanu ndi chiwiri uja awombe lipenga lake, chinsinsi cha Mulungu chidzachitika monga momwe analengezera kwa atumiki ake, aneneri.”

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 10:7
9 Mawu Ofanana  

Pakuti Ambuye Yehova sadzachita kanthu osawulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.


amene thambo la kumwamba liyenera kumlandira kufikira nthawi zakukonzanso zinthu zonse, zimene Mulungu analankhula za izo m'kamwa mwa aneneri ake oyera chiyambire.


Pakuti sindifuna, abale, kuti mukhale osadziwa chinsinsi ichi, kuti mungadziyese anzeru mwa inu nokha, kuti kuuma mtima kunadza pang'ono pa Israele, kufikira kudzaza kwa anthu amitundu kunalowa;


Ndipo kwa Iye amene ali wamphamvu yakukhazikitsa inu monga mwa Uthenga wanga Wabwino, ndi kulalikira kwa Yesu Khristu, monga mwa vumbulutso la chinsinsi chimene chinabisika mwa nthawi zonse zosayamba,


Ndipo ndinaona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nao Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu;


Pakuti Mulungu anapatsa kumtima kwao kuchita za m'mtima mwake, ndi kuchita cha mtima umodzi ndi kupatsa ufumu wao kwa chilombo, kufikira akwaniridwa mau a Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa