Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 10:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo ananena nane, Uyenera iwe kuneneranso pa anthu ndi mitundu, ndi manenedwe, ndi mafumu ambiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo ananena nane, Uyenera iwe kuneneranso pa anthu ndi mitundu, ndi manenedwe, ndi mafumu ambiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Pamenepo adandiwuza kuti, “Uyenera kulengezanso za mitundu yambiri ya anthu, za zilankhulo zosiyanasiyana, ndi za mafumu ambiri.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Ndipo anandiwuza kuti, “Iwe uyenera kulalikiranso za mitundu yambiri ya anthu, za mayiko, ziyankhulo ndi za mafumu.”

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 10:11
13 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzatengera dzikolo mau anga onse amene ndinanenera ilo, mau onse olembedwa m'buku ili, amene Yeremiya wanenera mitundu yonse.


Pamenepo anati kwa ine, Nenera kwa mafupa awa, nuti nao, Mafupa ouma inu, imvani mau a Yehova.


Ndipo anati kwa ine, Nenera kwa mpweya, nenera, wobadwa ndi munthu iwe, nuti kwa mpweya, Atero Ambuye Yehova, Idza, mpweya iwe, kuchokera kumphepo zinai, nuuzire ophedwa awa, kuti akhale ndi moyo.


Ndipo ndinatenga kabuku m'dzanja la mngelo, ndipo ndinakadya; ndipo kanali m'kamwa mwanga kozuna ngati uchi; ndipo pamene ndinakadya m'mimba mwanga mudawawa.


Ndipo anandipatsa ine bango ngati ndodo, ndi kuti, Tanyamuka, nuyese Kachisi wa Mulungu, ndi guwa la nsembe, ndi iwo akulambiramo.


Ndipo a mwa anthu ndi mafuko, ndi manenedwe, ndi mitundu apenyera mitembo yao masiku atatu ndi nusu lake, osalola mitembo yao iikidwe m'manda.


Ndipo ndinaona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nao Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu;


ndipo ali mafumu asanu ndi awiri asanu adagwa, imodzi iliko, yinayo siinadze; ndipo pamene ifika iyenera iyo kukhala kanthawi.


Ndipo nyanga khumi udaziona ndiwo mafumu khumi, amene sanalandire ufumu; koma alandira ulamuliro ngati mafumu, ora limodzi, pamodzi ndi chilombo.


Ndipo anena ndi ine, Madziwo udawaona uko akhalako mkazi wachigololoyo ndiwo anthu, ndi makamu, ndi mitundu, ndi manenedwe.


Ndipo aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa