Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 10:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo ndinatenga kabuku m'dzanja la mngelo, ndipo ndinakadya; ndipo kanali m'kamwa mwanga kozuna ngati uchi; ndipo pamene ndinakadya m'mimba mwanga mudawawa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo ndinatenga kabuku m'dzanja la mngelo, ndipo ndinakadya; ndipo kanali m'kamwa mwanga kozuna ngati uchi; ndipo pamene ndinakadya m'mimba mwanga mudawawa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Ndidalandira kampukutuko m'manja mwa mngelo uja, ndipo ndidadyadi. M'kamwamu kankazuna ngati uchi, koma nditakameza, m'mimbamu munkaŵaŵa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Ndinatenga kabukuko mʼdzanja la mngeloyo ndipo ndinadyadi. Mʼkamwa mwanga kankazuna ngati uchi, koma nditakameza, mʼmimbamu munkawawa.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 10:10
9 Mawu Ofanana  

Pomlingirira Iye pandikonde; ndidzakondwera mwa Yehova.


Mau anu azunadi powalawa ine! Koposa uchi m'kamwa mwanga.


Ndizo zifunika koposa golide, inde, golide wambiri woyengetsa; zizuna koposa uchi ndi zakukha za zisa zake.


Mau okoma ndiwo chisa cha uchi, otsekemera m'moyo ndi olamitsa mafupa.


naufunyulula pamaso panga; ndipo unalembedwa m'kati ndi kubwalo; munalembedwa m'mwemo nyimbo za maliro, ndi chisoni, ndi tsoka.


M'mwemo mzimu unandinyamula ndi kuchoka nane; ndipo ndinamuka wowawidwa, womyuka mtima; koma dzanja la Yehova linandigwirizitsa.


Nati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, dyetsa m'mimba mwako, nudzaze matumbo ako ndi mpukutu uwu ndakupatsawu. M'mwemo ndinaudya, ndi m'kamwa mwanga munazuna ngati uchi.


Ndipo ananena nane, Uyenera iwe kuneneranso pa anthu ndi mitundu, ndi manenedwe, ndi mafumu ambiri.


Ndipo ndinamuka kwa mngelo, ndi kunena naye, Ndipatse kabukuko. Ndipo ananena ndi ine, Dzatenge, nudye; ndipo kadzawawitsa m'mimba mwako, komatu m'kamwa mwako kadzazuna ngati uchi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa