Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 1:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo ndinacheuka kuona wonena mau amene adalankhula ndi ine. Ndipo nditacheuka ndinaona zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo ndinacheuka kuona wonena mau amene adalankhula ndi ine. Ndipo nditacheuka ndinaona zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolide;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Nditacheuka kuti ndiwone akundilankhula ndani, ndidaona ndodo zoikapo nyale zisanu ndi ziŵiri zagolide.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Nditatembenuka kuti ndione amene amandiyankhulayo, ndinaona zoyikapo nyale zisanu ndi ziwiri zagolide.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 1:12
11 Mawu Ofanana  

Ndipo uzipanga nyali zake, zisanu ndi ziwiri; ndipo ayatse nyali zake, ziwale pandunji pake.


Ndipo anapanga nyali zake zisanu ndi ziwiri ndi mbano zake, ndi zoolera zake, za golide woona.


Mau a Yehova aitana mzinda, ndi wanzeru aopa dzina lanu; tamverani ndodo, ndi Iye amene anaiika.


Ndipo anati kwa ine, Uona chiyani? Ndipo ndinati, Ndaona, taonani, choikaponyali cha golide yekhayekha, ndi mbale yake pamwamba pake, ndi nyali zake zisanu ndi ziwiri pamenepo; nyalizo zinali ndi misiwe isanu ndi iwiri, ndiyo ya nyalizo zinali pamwamba pake;


ndipo pakati pa zoikaponyalizo wina wonga Mwana wa Munthu atavala chofikira kumapazi ake, atamangira lamba lagolide pachifuwa.


Chifukwa chake lemba zimene unaziona, ndi zimene zilipo, ndi zimene zidzaoneka m'tsogolomo;


chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene unaziona padzanja langa lamanja, ndi zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide: nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndizo angelo a Mipingo isanu ndi iwiri; ndipo zoikaponyali zisanu ndi ziwiri ndizo Mipingo isanu ndi iwiri.


Kwa mngelo wa Mpingo wa ku Efeso lemba: Izi azinena Iye amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziwiri m'dzanja lake lamanja, Iye amene ayenda pakati pa zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide:


Zitatha izi ndinapenya, ndipo taonani, khomo lotseguka mu Mwamba, ndipo mau oyamba ndinawamva, ngati lipenga lakulankhula ndi ine, anati, Kwera kuno, ndipo ndidzakuonetsa zimene ziyenera kuchitika m'tsogolomo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa