Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Amosi 9:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo ndidzabwezanso undende wa anthu anga Israele, ndipo adzamanganso mizinda ya mabwinja, ndi kukhala m'menemo; nadzaoka minda ya mipesa nadzamwa vinyo wake, nadzalima minda ndi kudya zipatso zake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo ndidzabwezanso undende wa anthu anga Israele, ndipo adzamanganso mabwinja, ndi kukhala m'menemo; nadzaoka minda ya mipesa nadzamwa vinyo wake, nadzalima minda ndi kudya zipatso zake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 “Ndidzaŵabwezeranso pabwino anthu anga Aisraele. Adzamanganso mizinda yamabwinja ndi kumakhalamo. Adzalima minda ya mphesa ndipo adzamwa vinyo wake. Adzalima minda ndipo adzadya zipatso zake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Ndidzawabwezeranso pabwino anthu anga Aisraeli; mizinda imene inali mabwinja idzamangidwanso ndipo azidzakhalamo. Adzalima minda ya mpesa ndipo adzamwa vinyo wake; adzalima minda ndipo adzadya zipatso zake.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 9:14
31 Mawu Ofanana  

nafese m'minda, naoke mipesa, ndiyo yakubala zipatso zambiri.


Ha, chipulumutso cha Israele chichokere mu Ziyoni! Pakubweretsa Mulungu anthu ake a m'ndende, Yakobo adzakondwera, Israele adzasekera.


Tukula maso ako uunguzeunguze ndi kuona; iwo onse asonkhana pamodzi, adza kwa iwe; ana ako aamuna adzachokera kutali, ndi ana ako aakazi adzaleredwa pambali.


Ndipo iwo adzamanga mabwinja akale, nadzamanga pa miunda yakale, nadzakonzanso mizinda yopasuka, mabwinja a mibadwo yambiri.


Ndipo iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzaoka minda yampesa, ndi kudya zipatso zake.


Ndipo padzakhala kuti nditazula iwo, ndidzabwera, ndipo ndidzawachitira chisoni; ndipo ndidzabwezanso iwo, yense ku cholowa chake, ndi yense kudziko lake.


Koma, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israele kuchokera kudziko la kumpoto, ndi kumaiko ena kumene anawapirikitsirako; ndipo ndidzawabwezanso kudziko lao limene ndinapatsa makolo ao.


koma, Pali Yehova, amene anakweza ndi kutsogolera mbeu za nyumba ya Israele kuwatulutsa m'dziko la kumpoto, ndi kumaiko onse kumene ndinawapirikitsirako, ndipo adzakhala m'dziko lao.


Pakuti ndidzaika maso anga pa iwo kuti ndiwachitire iwo bwino, ndipo ndidzawabwezanso kudziko ili: ndipo ndidzamangitsa mudzi wao, osawapasula; ndi kuwabzala, osawazula iwo.


Ndipo ndidzapezedwa ndi inu, ati Yehova, ndidzabwezanso undende wanu, ndipo ndidzasonkhanitsa inu kwa mitundu yonse, ndi kumalo konse kumene ndinakupirikitsirani inu, ati Yehova; ndipo ndidzakubwezeraninso kumalo kumene ndinakutengani inu andende.


Atero Yehova: Taonani, ndidzabwezanso undende wa mahema a Yakobo, ndipo ndidzachitira chifundo zokhalamo zake, ndipo mzinda udzamangidwa pamuunda pake, ndi chinyumba chidzakhala momwe.


Pakuti, taona, masiku adzadza, ati Yehova, amene ndidzabwezanso undende wa anthu anga Aisraele ndi Ayuda, ati Yehova; ndipo ndidzawabwezera kudziko limene ndinapatsa makolo ao. Ndipo adzakhala nalo.


Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Kawirinso adzanena mau awa m'dziko la Yuda ndi m'mizinda yake, pamene ndibwezanso undende wao; Yehova akudalitse iwe, wokhalamo chilungamo, iwe phiri lopatulika.


Ndipo padzakhala kuti, monga ndayang'anira iwo kuzula ndi kupasula ndi kugwetsa, ndi kuononga ndi kusautsa; momwemo ndidzayang'anira iwo kumangitsa mudzi ndi kubzala, ati Yehova.


Ndiponso udzalima minda ya mpesa pa mapiri a Samariya; akuoka adzaoka, nadzayesa zipatso zake zosapatulidwa.


Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Nyumba ndi minda ndi minda yampesa idzagulidwanso m'dziko muno.


Taonani, ndidzawasokolotsa m'maiko monse, kumene ndinawapirikitsira ndi mkwiyo wanga, ndi m'kupsa mtima kwanga, ndi mu ukali waukulu, ndipo ndidzawabwezeranso kumalo kuno, ndipo ndidzawakhazikitsa mokhulupirika,


mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, chifundo chake nchosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.


Ndipo ndidzabweza undende wa Yuda ndi wa Israele, ndipo ndidzamangitsa mudzi wao, monga poyamba paja.


Ndipo ndidzabweza undende wao, undende wa Sodomu ndi ana ake, ndi undende wa Samariya ndi ana ake, ndi undende wa andende ako pakati pao;


Nadzakhalamo osatekeseka, nadzamanga nyumba, ndi kuoka mpesa m'mindamo, nadzakhalamo mosatekeseka, ndikatha kukwaniritsira maweruzo pa onse akuwapeputsa pozungulira pao; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao.


Nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga ana a Israele pakati pa amitundu kumene adankako, ndi kuwasokolotsa kumbali zonse, ndi kulowa nao m'dziko mwao;


Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Tsopano ndidzabweza undende wa Yakobo, ndi kuchitira chifundo nyumba yonse ya Israele, ndipo ndidzachitira dzina langa loyera nsanje.


Popeza tsono mupondereza aumphawi, ndi kumsonkhetsa tirigu; mwamanga nyumba za miyala yosema, koma simudzakhala m'mwemo; mwaoka minda ya mipesa yokonda, koma simudzamwa vinyo wake.


Ndipo zolemera zao zidzakhala zakufunkhidwa; ndi nyumba zao zabwinja; adzamangadi nyumba, koma sadzagonamo; adzaoka minda yampesa koma sadzamwa vinyo wake.


Ndipo dziko la kunyanja lidzakhala la otsala a nyumba ya Yuda; adzadyetsa zoweta zao pamenepo; madzulo adzagona m'nyumba za Asikeloni; pakuti Yehova Mulungu wao adzawazonda, nadzabweza undende wao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa