Amosi 6:10 - Buku Lopatulika10 Ndipo mbale wake wa munthu akamnyamula, ndiye womtentha, kutulutsa mafupa m'nyumba, nakati kwa iye ali m'kati mwa nyumbamo, Atsala wina nawe kodi? Nakati Iai; pamenepo adzati, Khala chete; pakuti sitingatchule dzina la Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Ndipo mbale wake wa munthu akamnyamula, ndiye womtentha, kutulutsa mafupa m'nyumba, nakati kwa iye ali m'kati mwa nyumbamo, Atsala wina nawe kodi? Nakati Iai; pamenepo adzati, Khala chete; pakuti sitingatchule dzina la Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Mbale wake wa wina mwa akufawo, woyenera kusamala za maliro, adzafika kudzatulutsa mtembo m'nyumbamo. Tsono adzafunsa wina amene watsalakobe m'nyumbamo kuti, “Kodi uli ndi winanso wamoyo m'menemo?” Iyeyo adzayankha kuti, “Ai mulibiretu.” Ndipo mbaleyo adzati, “Khala chete, iwe! Tisayerekeze kutchula dzina la Chauta.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Ndipo ngati mʼbale wake wa wina wakufayo, woyenera kusamala za maliro, adzafika kudzatulutsa mitembo mʼnyumbamo nʼkufunsa aliyense amene akubisalabe mʼnyumbamo kuti, “Kodi uli ndi wina wamoyo mʼmenemo?” Ndipo munthu wobisalayo ndi kuyankha kuti, “Ayi,” mʼbaleyo adzanena kuti, “Khala chete! Ife tisayerekeze kutchula dzina la Yehova.” Onani mutuwo |