Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Amosi 5:26 - Buku Lopatulika

26 Inde mwasenza hema wa mfumu yanu, ndi tsinde la mafano anu, nyenyezi ya mulungu wanu, amene mudadzipangira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Inde mwasenza hema wa mfumu yanu, ndi tsinde la mafano anu, nyenyezi ya mulungu wanu, amene mudadzipangira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Ndipotu muzidzanyamula Sakuti, mfumu yanu, ndi nyenyezi ija Kaiwani, mulungu wanu, mafano amene mudadzipangira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Inu mwanyamula kachisi wa mfumu yanu, ndi nyenyezi ija Kaiwani, mulungu wanu, mafano amene munadzipangira.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 5:26
7 Mawu Ofanana  

Nditero popeza iwo anandisiya, napembedza Asitaroti mulungu wa Asidoni, ndi Kemosi mulungu wa Amowabu, ndi Milikomu mulungu wa ana a Amoni, osayenda m'njira zanga, kuchita chimene chiyenera pamaso panga, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga, monga umo anatero Davide atate wake.


popeza ananyoza maweruzo anga, osayenda m'malemba anga, naipsa masabata anga; pakuti mitima yao inatsata mafano ao.


Ndipo usamapereka a mbumba yako kuwapitiriza kumoto chifukwa cha Moleki; usamaipsa dzina la Mulungu wako; Ine ndine Yehova.


M'mwemo ndidzakutengani kunka nanu kundende kutsogolo kwa Damasiko, ati Yehova, amene dzina lake ndiye Mulungu wa makamu.


Ndipo munatenga chihema cha Moleki, ndi nyenyezi ya mulungu Refani, zithunzizo mudazipanga kuzilambira; ndipo ndidzakutengani kunka nanu m'tsogolo mwake mwa Babiloni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa