Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Amosi 5:25 - Buku Lopatulika

25 Ngati munabwera nazo kwa Ine nsembe zophera ndi zaufa zaka makumi anai m'chipululu, inu nyumba ya Israele?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Ngati munabwera nazo kwa Ine nsembe zophera ndi zaufa zaka makumi anai m'chipululu, inu nyumba ya Israele?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 “Kodi inu anthu a ku Israele, zaka makumi anai zimene mudakhala m'chipululu, mudanditsirirako nsembe ndi kundipatsa mitulo?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 “Kodi pa zaka makumi anayi zimene munakhala mʼchipululu muja munkandibweretsera nsembe ndi zopereka, inu nyumba ya Israeli?

Onani mutuwo Koperani




Amosi 5:25
12 Mawu Ofanana  

Ngakhale apa atadzipangira mwanawang'ombe woyenga, nati, Suyu Mulungu wako anakukweza kuchokera ku Ejipito, nachita zopeputsa zazikulu;


Ndipo munawalera zaka makumi anai m'chipululu, osasowa kanthu iwo; zovala zao sizinathe, ndi mapazi ao sanatupe.


popeza ananyoza maweruzo anga, osayenda m'malemba anga, naipsa masabata anga; pakuti mitima yao inatsata mafano ao.


popeza sanachite maweruzo anga, koma ananyoza malemba anga, naipsa masabata anga, ndi maso ao anatsata mafano a atate ao.


Koma anapandukira Ine, osafuna kundimvera Ine, sanataye yense zonyansa pamaso pake, sanaleke mafano a Ejipito; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'dziko la Ejipito.


Ndipo asamapheranso milungu ina nsembe zao, zimene azitsata ndi chigololo. Ili liwakhalire lemba losatha mwa mibadwo yao.


Nena kwa anthu onse a m'dziko, ndi kwa ansembe, kuti, Muja mukasala ndi kulira mwezi wachisanu, ndi wachisanu ndi chitatu, zaka izi makumi asanu ndi awiri, kodi mukasalira Ine, Inedi?


Ndipo tsopano, opani Yehova ndi kumtumikira ndi mtima wangwiro ndi woona; nimuchotse milungu imene makolo anu anaitumikira tsidya lija la mtsinje, ndi mu Ejipito; nimutumikire Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa