Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Amosi 5:22 - Buku Lopatulika

22 Inde, mungakhale mupereka kwa Ine nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zaufa, sindidzazilandira Ine; ndi nsembe zoyamika za ng'ombe zanu zonenepa, sindidzazisamalira Ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Inde, mungakhale mupereka kwa Ine nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zaufa, sindidzazilandira Ine; ndi nsembe zoyamika za ng'ombe zanu zonenepa, sindidzazisamalira Ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Ngakhale mudzapereke nsembe zanu zopsereza ndiponso zaufa, Ine sindidzazivomera. Nsembe zanu zachiyanjano zophera ng'ombe zonenepa sindidzaziyang'ana nkomwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Ngakhale mupereke nsembe zopsereza ndi nsembe zachakudya, Ine sindidzazilandira. Ngakhale mupereke nsembe zabwino zachiyanjano, Ine sindidzaziyangʼana nʼkomwe.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 5:22
19 Mawu Ofanana  

Ndidzapereka kwa Inu nsembe yachiyamiko, ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova.


Nsembe ndi chopereka simukondwera nazo; mwanditsegula makutu. Nsembe yopsereza ndi yamachimo simunapemphe.


Wopereka nsembe yachiyamiko andilemekeza Ine; ndipo kwa iye wosunga mayendedwe ake ndidzamuonetsa chipulumutso cha Mulungu.


Nsembe ya oipa inyansa Yehova; koma pemphero la oongoka mtima limkondweretsa.


Nsembe ya oipa inyansa; makamaka pakudza nayo iwo mwachiwembu.


Nditani nazo nsembe zanu zochulukazo? Ati Yehova; ndakhuta nazo nsembe zopsereza za nkhosa zamphongo ndi mafuta a nyama zonenepa; sindisekera ndi mwazi wa ng'ombe zamphongo, ngakhale wa anaankhosa, ngakhale wa atonde.


Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwanawankhosa alingana ndi wothyola khosi la galu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza lubani akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zaozao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao;


Atero Yehova kwa anthu awa, Chomwecho akonda kusocherera; sanakanize mapazi ao; chifukwa chake Yehova sawalandira; tsopano adzakumbukira choipa chao, nadzalanga zochimwa zao.


Lubani andifumiranji ku Sheba, ndi nzimbe ku dziko lakutali? Nsembe zopsereza zanu sizindisekeretsa, nsembe zophera zanu sizindikondweretsa Ine.


Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele; Ikani zopereka zopsereza zanu pa nsembe zophera zanu, nimudye nyama.


Ndipo chilamulo cha nsembe zoyamika, zimene azibwera nazo kwa Yehova ndi ichi:


Mundichotsere phokoso la nyimbo zanu; sindifuna kumva mayimbidwe a zisakasa zanu.


Ndipo tsopano, mupepeze Mulungu, kuti atichitire chifundo; ichicho chichokera kwa inu; kodi Iye adzavomereza ena a inu? Ati Yehova wa makamu.


Ndipo Samuele anati, Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mau a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa