Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Amosi 5:20 - Buku Lopatulika

20 Kodi tsiku la Yehova silidzakhala la mdima, si la kuunika ai? Lakuda bii, lopanda kuwala m'menemo?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Kodi tsiku la Yehova silidzakhala la mdima, si la kuunika ai? Lakuda bii, lopanda kuwala m'menemo?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Kodi suja tsiku la Chauta ndi mdima wokhawokha osati kuŵala, kodi suja lili ngati usiku wabii wopanda mpoti mbee pomwe!

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Kodi tsiku la Yehova silidzakhala mdima osati kuwala, mdima wandiweyani, popanda powala pena paliponse?

Onani mutuwo Koperani




Amosi 5:20
13 Mawu Ofanana  

Chifukwa nyenyezi za kumwamba ndi makamu ao sizidzawala; dzuwa lidzada m'kutuluka kwake, ndipo mwezi sudzaonetsa kuwala kwake.


nadzayang'ana padziko, koma taonani, nkhawa ndi mdima, kuziya kwa nsautso; ndi mdima woti bii udzaingitsidwa.


Monga mbusa afunafuna nkhosa zake tsiku lokhala iye pakati pa nkhosa zake zobalalika, momwemo ndidzafunafuna nkhosa zanga; ndipo ndidzawalanditsa m'malo monse anabalalikamo tsiku la mitambo ndi la mdima.


tsiku la mdima, la mdima wandiweyani, tsiku la mitambo, mitambo yochindikira, ngati m'mbandakucha moyalika pamapiri; mtundu waukulu ndi wamphamvu, panalibe wotere ndi kale lonse, sipadzakhalanso wotere utapita uwu, kufikira zaka za mibadwo yambiri.


Pakuti tsiku la Yehova layandikira amitundu onse; monga unachita iwe, momwemo adzakuchitira; chochita iwe chidzakubwerera pamutu pako.


Koma ndi chigumula chosefukira adzatha konse malo ake, nadzapirikitsira adani ake kumdima.


Tsikulo ndi tsiku la mkwiyo, tsiku la msauko ndi lopsinja tsiku la bwinja, ndi chipasuko, tsiku la mdima ndi la chisisira, tsiku la mitambo ndi lakuda bii;


Pomwepo mfumu inati kwa atumiki, Mumange iye manja ndi miyendo, mumponye kumdima wakunja; komweko kudzali kulira ndi kukukuta mano.


Koma pomwepo, atapita masauko a masiku awo, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwake, ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndi mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka:


mafunde oopsa a nyanja, akuwinduka thovu la manyazi a iwo okha; nyenyezi zosokera, zimene mdima wakuda bii udazisungikira kosatha.


Ndipo wachisanu anatsanulira mbale yake pa mpando wachifumu wa chilombo; ndipo ufumu wake unadetsedwa; ndipo anatafuna malilime ao ndi kuwawa kwake,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa