Amosi 5:16 - Buku Lopatulika16 Chifukwa chake atero Yehova, Mulungu wa makamu, Ambuye, M'makwalala onse mudzakhala kulira, ndi m'miseu yonse adzati, Kalanga ine! Kalanga ine! Nadzaitana wakumunda adze kumaliro, ndi odziwa maliridwe a nthetemya alire. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Chifukwa chake atero Yehova, Mulungu wa makamu, Ambuye, M'makwalala onse mudzakhala kulira, ndi m'miseu yonse adzati, Kalanga ine! Kalanga ine! Nadzaitana wakumunda adze kumaliro, ndi odziwa maliridwe a nthetemya alire. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Nchifukwa chake zimene akunena Chauta, Ambuye, Mulungu Wamphamvuzonse, ndi izi: “M'mabwalo monse mudzakhala kulira, ndipo m'miseu monse anthu azidzangoti, ‘Mayo! Mayo!’ Ngakhale anthu wamba adzaŵaitana kuti adzalire, adzaitananso anthu odziŵa kubuma maliro kuti adzalire. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Choncho izi ndi zimene Ambuye, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, akunena: “Mʼmisewu monse mudzakhala kulira mofuwula, ndi kulira chifukwa cha kuwawa kwa masautso kudzakhala paliponse. Adzayitana alimi kuti adzalire, ndipo anthu odziwa maliridwe anthetemya adzalira mofuwula. Onani mutuwo |