Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 3:14 - Buku Lopatulika

14 Pakuti tsiku lakumlanga Israele chifukwa cha zolakwa zake, ndidzalanganso maguwa a nsembe a ku Betele; ndi nyanga za guwa la nsembe zidzadulidwa, ndipo zidzagwa pansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Pakuti tsiku lakumlanga Israele chifukwa cha zolakwa zake, ndidzalanganso maguwa a nsembe a ku Betele; ndi nyanga za guwa la nsembe zidzadulidwa, nizidzagwa pansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 “Pa tsiku limene ndidzalange Israele chifukwa cha zolakwa zake, maguwa a ku Betele ndidzaŵagumula, ndipo nyanga za guwa zidzathyoka nkugwa pansi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 “Pa tsiku limene ndidzalange Israeli chifukwa cha machimo ake, ndidzagumula maguwa ansembe a ku Beteli; nyanga za guwa zidzathyoka ndipo zidzagwa pansi.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 3:14
15 Mawu Ofanana  

Anagumulanso guwa la nsembe linali ku Betele, ndi msanje adaumanga Yerobowamu mwana wa Nebati wolakwitsa Israele uja; guwa la nsembelo, ndi msanje womwe anagumula; natentha msanje, naupondereza ukhale fumbi, natentha chifanizo.


Chitatha ichi chonse tsono, Aisraele onse opezekako anatuluka kunka kumizinda ya Yuda, naphwanya zoimiritsa, nalikha zifanizo, nagamula misanje ndi maguwa a nsembe mu Yuda monse, ndi mu Benjamini, mu Efuremunso, ndi mu Manase, mpaka adaziononga zonse. Pamenepo ana onse a Israele anabwerera, yense kudziko lake ndi kumizinda yao.


Ndipo tsopano, muka, tsogolera anthu kunka nao kumene ndinakuuza; taona, mthenga wanga akutsogolera; koma tsiku lakuwazonda Ine ndidzawalanga chifukwa cha kuchimwa kwao.


nagona pansi pa zofunda za chikole kumaguwa a nsembe ali onse, ndi m'nyumba ya Mulungu wao akumwa vinyo wa iwo olipitsidwa.


Idzani ku Betele, mudzalakwe ku Giligala, nimuchulukitse zolakwa, nimubwere nazo nsembe zanu zophera m'mawa ndi m'mawa, magawo anu akhumi atapita masiku atatuatatu;


Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Betele anatumiza kwa Yerobowamu mfumu ya Israele, ndi kuti, Amosi wapangira inu chiwembu pakati pa nyumba ya Israele; dziko silingathe kulola mau ake onse.


koma usaneneranso ku Betele; pakuti pamenepo mpamalo opatulika a mfumu, ndiyo nyumba yachifumu.


ndi misanje ya Isaki idzakhala bwinja; ndi malo opatulika a Israele adzapasuka; ndipo ndidzaukira nyumba ya Yerobowamu ndi lupanga.


Ndinaona Ambuye alikuima paguwa la nsembe, nati Iye, Kantha mitu ya nsanamira, kuti ziundo zigwedezeke; nuphwanye mitu yao yonse; ndipo ndidzapha otsiriza ao ndi lupanga; wothawayo mwa iwo sadzathawadi, ndi wopulumukayo mwa iwo sadzapulumukadi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa