Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 6:13 - Buku Lopatulika

13 Pakuti pamene Mulungu analonjezana naye Abrahamu, popeza analibe wamkulu woposa kumlumbira, analumbira pa Iye yekha,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Pakuti pamene Mulungu analonjezana naye Abrahamu, popeza analibe wamkulu woposa kumlumbira, analumbira pa Iye yekha,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Pamene Mulungu ankamulonjeza kanthu Abrahamu, adaalumbira kuti, “Pali Ine ndemwe, Mulungune.” Adaatero, popeza kuti panalibe wamkulu koposa Mwiniwakeyo amene akadamtchula polumbirapo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Pamene Mulungu ankamulonjeza Abrahamu, popeza panalibe wamkulu womuposa, amene akanamutchula ndikulumbira mwa Iye, analumbira mwa Iye yekha kuti,

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 6:13
15 Mawu Ofanana  

chipanganocho anapangana ndi Abrahamu, ndi lumbiro lake ndi Isaki;


Kumbukirani Abrahamu, Isaki ndi Israele, atumiki anu, amene munawalumbirira ndi kudzitchula nokha, amene munanena nao, Ndidzachulukitsa mbeu zanu ngati nyenyezi za kuthambo, ndi dziko ili lonse ndanenali ndidzapatsa mbeu zanu, likhale cholowa chao nthawi zonse.


Ndadzilumbira ndekha, mau achokera m'kamwa mwanga m'chilungamo, ndipo sadzabwerera, kuti mabondo onse adzandigwadira Ine, malilime onse nadzalumbira Ine.


Koma ngati simudzamva mau amenewa, Ine ndilumbira, pali Ine mwini, ati Yehova, nyumba iyi idzakhala yabwinja.


Chifukwa chake tamvani mau a Yehova, nonse Ayuda okhala m'dziko la Ejipito: Taonani, ndalumbira, Pali dzina langa lalikulu, ati Yehova, kuti dzina langa silidzatchulidwanso m'kamwa mwa munthu aliyense wa Yuda m'dziko la Ejipito, ndi kuti, Pali Yehova Mulungu.


Pakuti ndalumbira, Pali Ine ati Yehova, kuti Bozira adzakhala chizizwitso, chitonzo, chopasuka, ndi chitemberero; ndipo mizinda yake yonse idzakhala yopasuka chipasukire.


Ndidzaononganso nyama zake zonse za kumadzi ambiri; ndi phazi la munthu silidzavundulira, ndi ziboda za nyama zosawavundulira.


Mudzapatsa kwa Yakobo choonadi, ndi kwa Abrahamu chifundo chimene munalumbirira makolo athu kuyambira masiku a kale lomwe.


chilumbiro chimene Iye anachilumbira kwa Abrahamu atate wathu.


Abale, ndinena monga munthu. Pangano, lingakhale la munthu, litalunzika, palibe munthu aliyesa chabe, kapena kuonjezapo.


Pakuti ngati kulowa nyumba kuchokera kulamulo, sikuchokeranso kulonjezano; koma kumeneku Mulungu anampatsa Abrahamu kwaufulu mwa lonjezano.


Taonani, ndakupatsani dzikoli pamaso panu, lowani landirani dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuti ili ndidzawapatsa iwo ndi mbeu zao pambuyo pao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa