Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ahebri 11:39 - Buku Lopatulika

39 Ndipo iwo onse adachitidwa umboni mwa chikhulupiriro, sanalandire lonjezanolo,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 Ndipo iwo onse adachitidwa umboni mwa chikhulupiriro, sanalandira lonjezanolo,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 Anthu onseŵa, ngakhale adaaŵachitira umboni wokoma chifukwa cha chikhulupiriro chao, sadalandire zimene Mulungu adaalonjeza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 Onsewa anayamikidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo, komabe palibe wa iwo amene analandira zimene analonjezedwa.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 11:39
6 Mawu Ofanana  

Pakuti chikusowani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano.


Iwo onse adamwalira m'chikhulupiriro, osalandira malonjezano, komatu adawaona ndi kuwalankhula kutali, navomereza kuti ali alendo ndi ogonera padziko.


Pakuti momwemo akulu anachitidwa umboni.


Ndipo mwa ichi ali Nkhoswe ya chipangano chatsopano, kotero kuti, popeza kudachitika imfa yakuombola zolakwa za pa chipangano choyamba, oitanidwawo akalandire lonjezano la zolowa zosatha.


Kwa iwo amene kudavumbulutsidwa, kuti sanadzitumikire iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kuchokera Kumwamba; zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa