Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Aefeso 5:29 - Buku Lopatulika

29 pakuti munthu sanadane nalo thupi lake ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga, monganso Khristu Mpingo;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 pakuti munthu sanadana nalo thupi lake ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga, monganso Khristu Mpingo;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Palibiretu munthu amene amadana ndi thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulisamala bwino, monga momwe Khristu amachitira Mpingo wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Pakuti palibe amene amadana nalo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulisamalira bwino, monga momwe Khristu amachitira ndi mpingo wake

Onani mutuwo Koperani




Aefeso 5:29
13 Mawu Ofanana  

Ndipo anati Adamu, Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga, ndi mnofu wa mnofu wanga; ndipo adzatchedwa Mkazi, chifukwa anamtenga mwa mwamuna.


Wachifundo achitira moyo wake zokoma; koma wankhanza avuta nyama yake.


Chitsiru chimanga manja ake, ndipo chidya nyama yakeyake.


Iye adzadyetsa zoweta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa m'manja mwake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.


Ndi mitengo yakuthengo idzapereka zobala zao, ndi nthaka idzapereka zipatso zake, ndipo adzakhazikika m'dziko mwao; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, nditadula zomangira goli lao, ndi kuwalanditsa m'manja mwa iwo akuwatumikiritsa.


Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m'mapiko ake, koma inu simunafune ai!


Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?


opanda nzeru, osasunga mapangano, opanda chikondi cha chibadwidwe, opanda chifundo;


Koteronso amuna azikonda akazi ao a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha;


pakuti tili ziwalo za thupi lake.


Chifukwa cha ichi munthu azisiya atate ndi amai, nadzaphatikizana ndi mkazi wake; ndipo iwo awiri adzakhala thupi limodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa